Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikufuna kuti chuma chathu china kapena chuma chathu chonse chidzaperekedwe ku gulu la Yehova tikadzamwalira?
Pamene munthu wamwalira, sangalamulirenso mmene chuma chake chiyenera kuyendetsedwera. (Mlal. 9:5, 6) Choncho asanamwalire, anthu ambiri amalemba wilo kapena chikalata chofotokoza mmene chuma chawo chidzagawidwire. (2 Maf. 20:1) Kawirikawiri m’chikalatacho amalembamo munthu amene adzagawe chumacho munthu amene walemba wiloyo akadzamwalira. M’mayiko ambiri, a boma ndi amene amagawa chuma chamasiye ngati wiloyi sinalembedwe. Choncho, ngati tikufuna kuti chuma chathu china kapena chuma chathu chonse chidzaperekedwe ku gulu la Yehova tikadzamwalira, tiyenera kulemba wilo kapena chikalata chofotokoza zimenezi. Tiyeneranso kusankha mosamala munthu kapena bungwe limene lidzagawe chuma chathu.
Munthu kapena bungwe limene talisankha kuti lidzagawe chuma chathu amakhala ndi udindo waukulu kwambiri woonetsetsa kuti zonse za m’chikalatacho zikutsatiridwa. Kusonkhanitsa pamodzi chuma chamasiye ndiponso kuchigawa kwa anthu amene anatchulidwa mu wilo kumatenga nthawi yaitali makamaka ngati chumacho ndi chambiri. Chikalatachi chiyenera kulembedwa mwadongosolo kuti munthu amene akugawa chumachi asadzavutike kuchitsatira. Komanso, nthawi zambiri a boma amakhala ndi dongosolo lawo logawira chuma chamasiye. Si kuti ndi munthu aliyense mumpingo amene angakhale woyenera kugawa chuma chamasiye. Tiyenera kusankha munthu amene angathedi kugawa chumacho moyenera. Iye ayenera kukhala wodalirika ndiponso amene angatsatire zonse zimene talemba m’chikalata chathu.—Onani nkhani yakuti, “Kodi Mumasangalala ndi ‘Mwayi Wopereka Nawo Mphatso Zachifundo’”? mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2011.
Ngati Munthu Atakupemphani kuti Mudzagawe Chuma Chake: Ngati munthu wakupemphani kuti mudzagawe chuma chamasiye iyeyo akamwalira, choyamba muyenera kuona ngati mungakwanitsedi kugawa chuma chamasiyecho. (Luka 14:28-32) Munthuyo akamwalira, muyenera kudziwitsa anthu onse amene analembedwa m’chikalata cha kagawidwe ka chuma chamasiyecho. Kenako, mogwirizana ndi malamulo okupatsani mphamvu zogawa chumacho, gawani chumacho malinga ndi zimene zinalembedwa mu wilo. Munthu amene anapemphedwa kuti agawe chuma chamasiye ayenera kuonetsetsa kuti akutsatira zimene zinalembedwa mu wilo kaya chumacho n’chochepa kapena chambiri. Chuma chonse chimene chimaperekedwa ku bungwe lililonse la Mboni za Yehova n’chagulu la Yehova.—Luka 16:10; 21:1-4.