Ndandanda ya Mlungu wa September 10
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 10
Nyimbo Na. 104 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 12 ndime 1-8 ndi bokosi patsamba 96 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 42-45 (Mph. 10)
Na. 1: Ezekieli 43:13-27 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Limagwiritsa Ntchito Dzina la Yehova?—rs tsa. 329 ndime 1-3 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tilandire Mzimu Woyera? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Kuphunzira Baibulo Patokha Kumatithandiza Kukhala Atumiki Amphamvu. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 27 mpaka 32.
Mph. 10: Chida Chilichonse Chimene Chidzapangidwe Kuti Chikuvulaze Sichidzapambana. (Yes. 54:17) Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2010, tsamba 10 ndi 11, ndime 13 mpaka 15. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene Yehova anawathandizira pamene ankakumana ndi mayesero ovuta kwambiri. Werengani Yesaya 59:1.
Mph. 10: “Muzitsatira Njira Zimene Zingakhale Zothandiza Polalikira.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero