Muzitsatira Njira Zimene Zingakhale Zothandiza Polalikira
1. Kodi tingaphunzire chiyani pa njira zosiyanasiyana zimene Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito polalikira?
1 Akhristu oyambirira ankalalikira uthenga wabwino kwa anthu a zikhalidwe komanso zipembedzo zosiyanasiyana. (Akol. 1:23) Ngakhale kuti onse ankalalikira uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu, iwo ankagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana malinga ndi anthu amene akuwalalikira. Mwachitsanzo, pamene Petulo ankalalikira kwa Ayuda amene ankalemekeza kwambiri Malemba, anayamba ndi kugwira mawu a mneneri Yoweli. (Mac. 2:14-17) Chitsanzo china ndi cha mmene Paulo analalikirira Agiriki chimene chili pa Machitidwe 17:22-31. Masiku anonso, m’madera ena anthu amalemekeza Malemba ndipo timatha kuwawerengera Baibulo pamene tikulalikira nyumba ndi nyumba. Komabe tiyenera kukhala osamala kwambiri tikamalalikira anthu amene si Akhristu, amene sakhulupirira Baibulo kapenanso amene sakonda zachipembedzo.
2. Kodi tingagawire bwanji mabuku mogwira mtima tikamalalikira anthu amene amakhulupirira Baibulo komanso amene salikhulupirira?
2 Muzifotokoza Mogwira Mtima Pogawira Mabuku: Chaka chautumiki chino mabuku ogawira azisintha pa miyezi iwiri iliyonse ndipo tizigawira magazini, timapepala ndi timabuku. Ngakhale anthu ambiri m’gawo lathu atakhala kuti sakhulupirira Baibulo, tingakambirane nawo nkhani imene ingawasangalatse kuchokera m’magazini, timapepala kapena timabuku. Mwina sitingawerenge nawo Baibulo pa ulendo woyamba kapena kutchula mwachindunji vesi la m’Baibulo. Koma anthuwo akasonyeza chidwi, tiziyesetsa kupanga ulendo wobwereza n’cholinga chakuti tiwathandize kuti azikhulupirira Mlengi ndiponso Baibulo. Koma tikamalalikira m’gawo limene anthu amakhulupirira Baibulo tingagwiritse ntchito mabuku athu ndiponso njira zimene zingakhale zothandiza. Ndipotu tikhoza kugawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena timabuku takuti, Mverani Mulungu kapenanso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Tingachite zimenezi ngakhale kuti mwezi umenewo sitikugawira mabukuwa. Cholinga chathu ndi kutsatira njira zimene zingakhale zothandiza polalikira.
3. Kodi mitima ya anthu a m’gawo lathu ndi yofanana bwanji ndi nthaka?
3 Konzani Nthaka: Mtima wa munthu uli ngati nthaka. (Luka 8:15) Nthaka ina imafunika kuikonza kwambiri tisanabzalepo mbewu za choonadi cha m’Baibulo kuti mbewuzo zimere mizu ndiponso kuti zikule. Akhristu oyambirira anakwanitsa kubzala mbewu ya choonadi panthaka yosiyanasiyana ndipo zimenezi zinawathandiza kukhala osangalala. (Mac. 13:48, 52) Ngati nafenso tingakhale ndi mtima umenewu zinthu zikhoza kutiyendera bwino.