Ndandanda ya Mlungu wa May 13
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 13
Nyimbo Na. 116 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 23 ndime1-8 ndi bokosi patsamba 180 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yohane 5-7 (Mph. 10)
Na. 1: Yohane 6:22-40 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi N’chifukwa Chiyani Zinali Zoyenera Kuti Dipo Liperekedwe M’njira Imene Linaperekedwera?—rs tsa. 122 ndime 6–tsa. 123 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingatsatire Bwanji Mfundo Yopezeka pa Numeri 15:37-40? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Mabuku Ogawira M’mwezi wa May ndi June. Nkhani. Fotokozani mwachidule chifukwa chake timapepala timeneti tili tabwino kwambiri m’gawo lanu. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza mmene wofalitsa angagawirire timapepalati polalikira kunyumba ndi nyumba.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 5:11, 12 ndi Mateyu 11: 16-19. Kambiranani mmene malemba amenewa angatithandizire mu utumiki wathu.
Mph. 10: “N’chiyani Chimatilimbikitsa kuti Tizilalikira?” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 91 ndi Pemphero