Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/13 tsamba 1
  • N’chiyani Chimatilimbikitsa kuti Tizilalikira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chiyani Chimatilimbikitsa kuti Tizilalikira?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Tanthauzo la Kukonda Mnansi Wathu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • “Uzikonda Mnzako Mmene Umadzikondera Wekha”
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kodi Chikondi Chanu N’chosefukira Motani?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kodi ‘Mumakonda Anzanu Ngati Mmene Mumadzikondera Nokha’?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 5/13 tsamba 1

N’chiyani Chimatilimbikitsa kuti Tizilalikira?

1. N’chiyani chimatilimbikitsa kuti tizilalikira?

1 Kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi ntchito yofunika kwambiri imene tiyenera kugwira masiku ano. Kugwira ntchito imeneyi kumasonyeza kuti timamvera malamulo awiri aakulu koposa omwe amatilamula kuti tizikonda Yehova komanso anthu. (Maliko 12:29-31) Chikondi n’chimene chimatilimbikitsa kukhala akhama pa ntchito yolalikira.—1 Yoh. 5:3.

2. Kodi tikamalalikira, timasonyeza bwanji kuti timakonda Yehova?

2 Kukonda Yehova: Kukonda Yehova, yemwe ndi Bwenzi lathu lapamtima, kumatilimbikitsa kuti tizilankhula za iye. Satana wakhala akunyoza Yehova kwa zaka pafupifupi 6,000. (2 Akor. 4:3, 4) Choncho, anthu amakhulupirira kuti Mulungu amaotcha anthu oipa kumoto. Amakhulupiriranso kuti Mulungu ndi Utatu ndiponso kuti iye sakonda anthu. Anthu ambiri afika ponena kuti Mulungu kulibe. Timalakalaka kuti anthu adziwe zoona zokhudza Atate wathu wakumwamba ameneyu. Iyetu amasangalala kwambiri tikamachita khama pa ntchito yolalikirayi, koma Satana sasangalala m’pang’ono pomwe.—Miy. 27:11; Aheb. 13:15, 16.

3. Kodi utumiki wathu umasonyeza bwanji kuti timakonda anthu?

3 Kukonda Anthu Anzathu: Nthawi iliyonse imene timalalikira munthu, timasonyeza kuti timamukonda. Anthu akulakalaka kumva uthenga wabwino m’nthawi yovuta ino. Anthu ambiri ali ngati anthu a ku Nineve omwe ‘sankadziwa kusiyanitsa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.’ (Yona 4:11) Utumiki wathu umaphunzitsa anthu mmene angakhalire ndi moyo wabwino komanso wosangalala. (Yes. 48:17-19) Uthenga umene timalalikira umawapatsa chiyembekezo. (Aroma 15:4) Ngati atamvetsera komanso kutsatira zimene aphunzirazo, “adzapulumuka.”—Aroma 10:13, 14.

4. N’chiyani chimene Yehova sadzaiwala?

4 Ana akhalidwe labwino amayesetsa kusonyeza kuti amakonda makolo awo nthawi zonse osati mwa apo ndi apo. Chifukwa chokonda kwambiri Mulungu komanso anthu, sitilalikira pa masiku amene timalowa mu utumiki okha koma timagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti tilalikire. Sitidzasiya kulalikira uthenga wabwino. (Mac. 5:42) Yehova sadzaiwala chikondi choterechi.—Aheb. 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena