Ndandanda ya Mlungu wa May 20
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 20
Nyimbo Na. 78 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 23 ndime 9-15 ndi mabokosi patsamba 184 ndi 186 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yohane 8-11 (Mph. 10)
Na. 1: Yohane 8:12-30 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Tingatani Kuti Tisanyengedwe Ndi Anthu Ophunzitsa Zonama?—Aroma 16:17; 2 Yoh. 9-11 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi N’chifukwa Chiyani Mulungu Sanangolamula Kuti Onse Amene Azimumvera Adzakhala ndi Moyo Kosatha?—rs tsa. 123 ndime 2–tsa. 124 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Njira Zowonjezera Utumiki Wanu—Mbali Yachitatu. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Gulu, tsamba 116, ndime 1 mpaka tsamba 117 ndime 1. Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri amene anagwirapo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ngati alipo. Kodi n’chiyani chinawasangalatsa pochita utumikiwu?
Mph. 10: Yehova Amatithandiza Kukwaniritsa Utumiki Wathu. (Eks. 4:10-12; Afil. 4:13) Nkhani yokambirana yochokera m’Buku Lapachaka, tsamba 102, ndime 1 ndiponso tsamba 112, ndime 1 mpaka 3. Pemphani abale ndi alongo kuti afotokoze zimene aphunzirapo pa nkhanizi.
Mph. 10: “Kodi Ndi Ndani Amene Angakonde Magazini Awa?” Mafunso ndi mayankho. Pemphani abale ndi alongo kuti atchule anthu ogwira ntchito zina kapena anthu ogwira ntchito m’boma omwe ali m’gawo lawo amene angapindule ndi nkhani inayake imene ili m’magazini athu.
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero