Ndandanda ya Mlungu wa July 22
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 22
Nyimbo Na. 23 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 26 ndime 9-15 ndi bokosi patsamba 208 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 22–25 (Mph. 10)
Na. 1: Machitidwe 22:17-30 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Tinganene Kuti Sitili Mbali ya Dziko Ngakhale Kuti Timakhala M’dzikoli?—Yoh. 17:15, 16 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi N’zotheka Kuti Akhristu Apite Kumwamba ndi Matupi Awo Enieni?—rs tsa. 214 ndime 4 mpaka tsa. 215 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Kodi Mwawakonzekera Bwanji Mavuto a ku Sukulu? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera atchule mavuto amene Akhristu achinyamata amakumana nawo kusukulu. Fotokozani mmene makolo angagwiritsire ntchito Watchtower Publications Index, mabuku a Zimene Achinyamata Amadzifunsa, webusaiti yathu ndi mabuku ena pa Kulambira kwa Pabanja kuti athandize ana awo kulimbana ndi mayesero amene amakumana nawo kusukulu komanso kuti azitha kufotokoza zimene amakhulupirira. (1 Pet. 3:15) Sankhani nkhani imodzi kapena ziwiri, ndipo fotokozani mfundo zina zothandiza zimene zili m’mabuku athu. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene ankachita kuti azitha kulalikira kusukulu.
Mph. 20: “Njira Zatsopano Zolalikirira M’malo Opezeka Anthu Ambiri.” Mafunso ndi mayankho. Fotokozani zimene mpingo wakonza pa ntchito yolalikira m’malo amene mumapezeka anthu ambiri pogwiritsa ntchito matebulo kapena mashelefu amatayala, ndipo tchulani zitsanzo zofotokoza mmene ntchitoyi ikuyendera m’madera ena.
Nyimbo Na. 95 ndi Pemphero