Ndandanda ya Mlungu wa August 19
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 19
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero.
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 27 ndime 19-26 ndi mabokosi a patsamba 212, 214 ndi 217 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Aroma 9–12 (Mph. 10)
Na. 1: Aroma 9:19-33 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Ngati Wina Wanena Kuti, ‘Kodi Mumakhulupirira Kuti Akhristu Okhulupirika Adzatengedwa Ndi Matupi awo N’kukakumana ndi Ambuye M’mlengalenga?’—rs tsa. 217 ndime 5-tsa. 218 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Baibulo Limapereka Zifukwa Ziti Zimene Sitiyenera Kuopa Anthu?—Luka 12:4-12 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: “Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya.” Mafunso ndi mayankho.
Mph. 10: Zimene Tinganene Kwa Anthu Amene Sakufuna Kuti Tiwalalikire. Nkhani yokambirana yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani zinthu ziwiri kapena zitatu zimene anthu a m’dera lanu amakonda kunena akafuna kuti musawalalikire, zomwe sizinatchulidwe m’buku la Kukambitsirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene tingayankhire kwa anthu oterewa. Chitani chitsanzo chimodzi.
Mph. 10: Muzilalikira Molimba Mtima. (Mac. 4:29) Nkhani yokambirana yochokera m’Buku Lapachaka la 2013, tsamba 49 ndime 1 mpaka 6 ndi tsamba 69 ndime 1 mpaka 6. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero