Ndandanda ya Mlungu wa September 23
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 23
Nyimbo Na. 66 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 1 ndime 8-14 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Akorinto 8-13 (Mph. 10)
Na. 1: 2 Akorinto 10:1-18 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Ngati Wina Wanena Kuti, ‘Ndimakhulupirira Kuti Munthu Akafa Amakabadwanso Kwinakwake’—rs tsa. 178 ndime 2-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Lemba la 1 Akorinto 10:13 Limatanthauza Chiyani? (Mph. 5 )
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: “Ndilandira Mabuku Anuwo, Inunso Mukalandira Athu.” Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anayankhira munthu amene analankhulapo mawu ngati amenewa munthuyo n’kukhutira.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chatha? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani zimene mpingo wanu unachita mu utumiki m’chaka chautumiki chathachi, makamaka zinthu zabwino zimene unakwanitsa kuchita, ndipo yamikirani abale ndi alongo. Tchulani mfundo imodzi kapena ziwiri zimene mpingo wanu uyenera kuwongolera chaka chimene talowachi, ndipo fotokozani zimene zingathandize mpingo wanuwo kuti mukwanitse kuzichita.
Mph. 15: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Machitidwe 16:19-40. Kambiranani mmene malemba amenewa angatithandizire mu utumiki. Mukambiranenso Zochitika mu Utumiki Wakumunda m’mwezi wa September 2013 zomwe zili patsamba 4.
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero