“Ndilandira Mabuku Anuwo, Inunso Mukalandira Athu”
N’kutheka kuti tinakumanapo ndi anthu ena amene anatiuza mawu ngati amenewa. Ndiye popeza sitilandira mabuku a zipembedzo omwe amanena zabodza, kodi tingamuyankhe bwanji munthu woteroyo mozindikira? (Aroma 1:25) Tinganene kuti: “Zikomo kwambiri. Koma kodi kapepala kanuka [kapena magazini yanuyi] kakufotokoza kuti mavuto amene anthu akukumana nawo adzatha bwanji? [Yembekezani kuti ayankhe. Ngati anganene kuti yankho la funso lanulo mulipeza mukawerenga kapepala kakeko, mukumbutseni zoti inuyo munamufotokozera kaye zimene zili m’magazini athu musanapemphe kuti mumugawire. Kenako werengani kapena nenani mawu a pa lemba la Mateyu 6:9, 10.] Yesu ananena kuti Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti chifuniro chake chichitike padziko lapansi. Choncho mabuku a chipembedzo amene ndimawerenga ndi omwe amagogomezera za Ufumu wa Mulungu umenewo. Kodi ndingakusonyezeni m’Baibulo zinthu zina zimene Ufumu wa Mulungu udzachite?