Kodi Likuoneka Bwanji?
Limeneli ndi funso labwino kwambiri kudzifunsa tikamafuna kugawira buku lililonse? Buku lililonse limene layamba kupindika m’makona, kuchoka mtundu wake, kuda kapena kung’ambika silipereka chithunzi chabwino cha gulu lathu ndipo likhoza kulepheretsa mwininyumba kumva uthenga wabwino ndiponso wopulumutsa moyo womwe uli m’mabukuwo.
Kodi tingatani kuti mabuku athu azikhala ooneka bwino? Anthu ambiri amaona kuti n’zothandiza kukonza zoti m’chikwama chawo cha mu utumiki, mabuku a mtundu umodzi azikhala pamodzi. Mwachitsanzo, amakhala ndi malo a mabuku, magazini, mabulosha ndipo mbali ina mathirakiti ndi zina zotero. Akamabwezera Baibulo ndi mabuku ena onse pamalo ake, amawaika mosamala kwambiri kuti asaonongeke. Ofalitsa ena amaika mabuku awo mu zinthu zina kapena m’mapepala a pulasitiki. Kaya tikusunga mabuku athu motani, tiyeni tiyesetse kupewa kugawira munthu mabuku owonongeka chifukwa zimenezi zingamupatse chifukwa chomveka chokanira uthenga wathu.—2 Akor. 6:3.