Kodi Mudzachita Zotani pa Nthawi ya Holide?
Nthawi ya maholide achipembedzo komanso aboma imakhala yabwino kulalikira chifukwa anthu ambiri amapezeka panyumba. Choncho mipingo ikulimbikitsidwa kuti ikonze dongosolo lodzalowa mu utumiki nthawi ya holide. Mukhoza kulengeza pa Msonkhano wa Utumiki ngati mpingo wakonza dongosolo lililonse lapadera lolowa mu utumiki pa nthawi ya holide. Mungachitenso bwino kulimbikitsa aliyense amene angakwanitse kumalowa nawo mu utumiki pa nthawiyi. N’zoona kuti nafenso timafunikira kupuma komanso kuchita zinthu zathu pa nthawi ya holide. Komabe tingachite bwino kupatula nthawi yolowa mu utumiki. Kuchita nawo utumiki pa nthawi ya holide kungakuthandizeni kuti mukhale wosangalala.—Mat. 11:29, 30.