Ndandanda ya Mlungu wa November 4
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 4
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 3 ndime 1-6 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Tito 1-3 mpaka Filimoni 1-25(Mph. 10)
Na. 1: Tito 2:1-15 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mumaona Kuti N’zoyenera Kukhala M’chipembedzo Chinachake?—rs tsa. 87 ndime 2—tsa. 88 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Sitiyenera ‘Kumvetsera Nkhani Zonama’?—1 Tim. 1:3, 4; 2 Tim. 4:3, 4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu November. Nkhani yokambirana pogwiritsa ntchito mafunso otsatirawa: Ngati pakufunikira, n’chifukwa chiyani tiyenera kugawiranso magazini pa masiku a Loweruka ndi Lamlungu amene tikugawira kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38? Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse kuti tigawire kapepalaka pamodzi ndi magazini? Kodi tinganene zotani kuti tiyambe kukambirana ndi munthuyo zokhudza magaziniwo pambuyo pomugawira kapepalaka. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire magazini iliyonse pamodzi ndi kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu. (Aheb. 4:12) Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2013, tsamba 57 ndime 1 mpaka tsamba 59 ndime 3. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene aphunzirapo.
Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero