“Tabwera Kuti . . . ”
Nthawi zambiri tikafika pakhomo la munthu, munthuyo amadabwa kuti ndife ndani, ndipo tabwera kudzatani. Ndiye kodi tinganene mawu ati kuti asatidabwe? Tikalonjerana, mwina tingayambe ndi mawu akuti, “Tabwera kuti . . . ” Mwachitsanzo tinganene kuti: “Tabwera kuti tikambirane za vuto limene likudetsa nkhawa anthu ambiri kudera lathu lino. Kodi mukuganiza kuti . . . ” Kapena tinganene kuti, “Tabwera kuti tikusonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo ndi anthu kwaulere.” Tikamanena mwamsanga chifukwa chimene tafikira pakhomo la anthu, anthuwo angakhale ndi chidwi chomvetsera zimene tikufuna kuwauza.