Ndandanda ya Mlungu wa November 25
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 25
Nyimbo Na. 52 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 4 ndime 1 mpaka 8 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yakobo 1-5 (Mph. 10)
Na. 1: Yakobo 1:22 mpaka 2:1-13 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Chikondi Chimathandiza Bwanji Munthu Kuti Asakhale Ndi Mantha?—1 Yoh. 4:16-18. (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kuwerenga Baibulo Kokha Sikokwanira?—rs tsa. 89 ndime 1-2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu December. Nkhani yokambirana. Kwa nthawi yosapitirira mphindi imodzi, fotokozani chifukwa chake magaziniwo angakhale othandiza m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani yoyambirira ya mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani yapachikuto m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo, mungachitenso zimenezi ndi nkhani ina imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire magazini iliyonse.
Mph. 10: Kodi Mungayankhe Bwanji? Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 69 ndime 1 mpaka 5. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuthandiza wophunzira Baibulo, yemwe akufuna kupanga chosankha pa nkhani inayake. Wophunzirayo akufunsa kuti, “Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?”
Mph. 10: “Nkhani Zothandiza mu Utumiki.” Mafunso ndi mayankho. Pogwiritsa ntchito nkhani yaposachedwapa yochokera pamutu wakuti “Kucheza Ndi Munthu Wina,” chitani chitsanzo mwachidule chosonyeza mfundo zimene zili m’ndime 3.
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero