Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Msonkhano
1. Kodi ntchito yoitanira anthu ku msonkhano wachigawo wa 2014 idzayamba liti?
1 Ngati mwakonza chakudya chapadera komanso chodula, ndipo mukufuna kuti anthu a m’banja lanu komanso anzanu adye chakudyacho, n’zodziwikiratu kuti mungawaitane mwansangala n’cholinga choti asalephere kudzadya chakudyacho. N’chimodzimodzinso ndi msonkhano wachigawo wa chaka chino. Pali zambiri zimene zachitika pokonzekera phwando lauzimu limeneli. Kutatsala milungu itatu kuti msonkhano wanu uyambe, mudzakhala ndi mwayi wogwira ntchito yoitanira anthu ku msonkhanowu. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tidzaitanire anthu kumsonkhanowu mwansangala, n’cholinga choti asadzalephere kubwera?
2. Kodi tiyenera kuganizira mfundo ziti, zomwe zidzatithandize kuti tidzagwire mwakhama ntchito yoitanira anthu kumsonkhano?
2 Kuganizira mmene chakudya chauzimu chimene Yehova amatipatsa pa misonkhano yachigawo chimatithandizira ifeyo patokha, kungachititse kuti tidzaone kufunika kogwira nawo ntchitoyi mwakhama. (Yes. 65:13, 14) Tisaiwalenso kuti ntchito yoitanira anthu ku msonkhano, yomwe imachitika chaka chilichonse, imakhala ndi zotsatira zabwino. Anthu ena amene tidzawaitanire kumsonkhawu, adzabweradi. Komabe ngakhale zitakhala kuti anthu ambiri sadzabwera, tikadzagwira ntchitoyi, zidzachititsa kuti Yehova alemekezeke komanso zidzasonyeza kuti iye ndi wowolowa manja.—Sal. 145:3, 7; Chiv. 22:17.
3. Kodi tizidzagawira bwanji timapepala toitanira anthu kumsonkhano?
3 Bungwe la akulu lililonse liyenera kuona njira yabwino imene mpingo wawo ungatsatire pogawira timapepalati. Angaonenso ngati pakufunika kuti ofalitsa azisiya kapepala pakhomo lomwe sanapezepo anthu kapena ngati pakufunika kuti azipereka kapepalaka kwa anthu, m’malo opezeka anthu ambiri m’gawo lawo. Kumapeto kwa mlungu tingagawire kapepalaka limodzi ndi magazini, ngati tapeza anthu achidwi. Ngati pa nthawi yogawira timapepalati, Loweruka lina lidzakhale Loweruka loyamba la mwezi, mudzagawire timapepalati pa tsikuli m’malo moyambitsa maphunziro a Baibulo. Ntchito yogawira timapepalati ikadzatha, tidzasangalala kwambiri podziwa kuti tagwira nawo mwakhama ntchitoyi ndipo tayesetsa kuitanira anthu ambiri kuphwando lauzimu lomwe Yehova wakonza.