“Khalani Ndi Khalidwe Labwino Pakati pa Anthu a M’dzikoli”
1. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tidzasonyeze khalidwe labwino pa nthawi ya msonkhano ukubwerawu?
1 Chaka chilichonse tikamachita msonkhano wachigawo, anthu savutika kuzindikira zimenezi. Choncho ndi bwino kuti khalidwe lathu lizikhala logwirizana ndi Mulungu amene timamulambira. (Lev. 20:26) Khalidwe komanso kavalidwe kathu, zizisonyeza kuti ndife otsatira enieni a Khristu. Pa nthawi ya msonkhano wachigawo kapena wa mayiko ukubwerawu, kodi tingatani kuti ‘tidzasonyeze khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli,’ zomwenso zidzalemekeze Atate wathu wakumwamba?—1 Pet. 2:12.
2. Kodi pa nthawi ya msonkhano wachigawo, tingadzasonyeze makhalidwe achikhristu m’njira ziti?
2 Mudzasonyeze Makhalidwe Oyenera Mkhristu: Tikamakondana komanso kuchitira zabwino “anthu akunja,” timasonyeza kuti ndife osiyana ndi dzikoli. (Akol. 3:10; 4:5; 2 Tim. 3:1-5) Tiyenera kukhala okoma mtima komanso oleza mtima tikamachita zinthu ndi akuluakulu a m’mahotelo kapena ogwira ntchito m’malesitilanti. Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale pa nthawi imene pabuka vuto linalake. Khalidwe labwino limaphatikizaponso kusiya kandalama kothokoza anthu ogwira ntchito palesitilanti, ngati anthu a kudera lathu amachita zimenezi.
3. Kodi makolo akukumbutsidwa kudzachita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani ayenera kudzachita zimenezi?
3 Makolo ayenera kumadzayang’anira ana awo pamalo a msonkhano, kumalesitilanti komanso kumalo ena. (Miy. 29:15) Woyang’anira wa pahotelo inayake anauza banja lina kuti: “Anthu inu timakukondani kwabasi. Ndinu anthu a makhalidwe abwino, ndi ana anu omwe. Anthu onse ogwira ntchito pahotelo pano akukamba za inu, ndipo tikulakalaka mutamabwera kumapeto kwa mlungu uliwonse.”
4. Pa nthawi ya msonkhano wachigawo, kodi ndi zinthu ziti zokhudza kavalidwe zomwe tiyenera kuziganizira?
4 Muzidzavala Modzilemekeza: Tikakhala pamalo a msonkhano tiyenera kuvala moyenera ndi modzilemekeza, osati motengera masitayilo a m’dzikoli. (1 Tim. 2:9) Ngakhale pamene tili kuhotelo kapena pamene tikupuma pambuyo pa pulogalamu ya tsikulo, sitiyenera kuvala motailira kapena kuvala zovala zolemba mawu osakhala bwino. Kuvala moyenera kudzachititsa kuti tisadzachite manyazi kuvala mabaji a msonkhano komanso kulalikira mwamwayi. Kuvala bwino ndiponso khalidwe lathu labwino pamene tili kumsonkhano, zidzathandiza kuti anthu a mitima yabwino amvetsere uthenga wa m’Baibulo komanso kuti alemekeze Yehova.—Zef. 3:17.