Ndandanda ya Mlungu wa June 9
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 9
Nyimbo Na. 51 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 12 ndime 14-19 ndi bokosi patsamba 148 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 1-5 (Mph. 10)
Na. 1: Levitiko 4:16-31 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Amene Baibulo Limawatcha “Oyera Mtima”—rs tsa. 331 ndime 1–tsa. 332 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuvala Ndiponso Kudzisamalira Moyenera?—lv tsa. 56 ndime 11-13 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Kodi Mwaziyesa? Nkhani yokambirana. Kambani nkhani yachidule yofotokoza mfundo zomwe zili m’nkhani izi, zomwe zinatuluka mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa posachedwapa: “Njira Zatsopano Zolalikirira M’malo Opezeka Anthu Ambiri” (km 7/13), “Kodi Tingawathandize Bwanji?” (km 12/13) ndi yakuti, “Tingathe Kuyambitsa Phunziro kwa Anthu Amene Timawapatsa Magazini” (km 1/14). Pemphani omvera kuti afotokoze phindu limene apeza pogwiritsa ntchito mfundo zomwe zili m’nkhani zimenezi.
Mph. 15: “Mwezi wa August Udzakhala Wosaiwalika.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Ngati timapepala takuti, Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo? tilipo, perekani kapepala kamodzi kwa aliyense, ndipo kambiranani zomwe zili m’kapepalako. Fotokozani zimene mpingo wakonza, kuti mudzathe kugawira timapepalati m’gawo lanu lonse.
Nyimbo Na. 107 ndi Pemphero