Ndandanda ya Mlungu wa June 23
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 23
Nyimbo Na. 112 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 13 ndime 1-7 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 10-13 (Mph. 10)
Na. 1: Levitiko 12:1-8 mpaka 13:1-8 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Zoona Zake za Kulambira Zinthu Zakale ndi Zifanizo za “Oyera Mtima”—rs tsa. 333 ndime 1–tsa. 334 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Yehova Amadana ndi Mawu Otukwana—lv tsa. 136-137 ndime 9-12 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Mabuku Ogawira M’mwezi wa July. Nkhani yokambirana. Fotokozani mwachidule zimene zili m’timabukuto. Kenako chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza mmene tingagawirire timabukuti.
Mph. 20: “Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Omwe Sadziwa Kuwerenga Komanso Amene Amavutika Kuwerenga?” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 55 ndi Pemphero