Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/14 tsamba 3-4
  • Kuphunzira Patokha N’kothandiza Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzira Patokha N’kothandiza Kwambiri
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Timitu
  • Pamafunika Kukonzekeretsa Maganizo
  • Mmene Tingaphunzirire
  • Zimene Tingaphunzire
  • ‘Mangani Banja Lanu’
  • Phindu Limene Tingapeze
Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
km 6/14 tsamba 3-4

Kuphunzira Patokha N’kothandiza Kwambiri

Kodi kuphunzira n’kutani? Kuphunzira si kungowerenga nkhani mwachisawawa. Kumafuna kuganizira mozama zimene ukuwerengazo, kuyesetsa kuzimvetsa, kuziyerekezera ndi zimene ukuzidziwa kale komanso kuona chifukwa chake zili choncho. Tikamaphunzira, tiziganizira mozama mfundo zimene tikuona kuti n’zatsopano kwa ifeyo. Tiziganiziranso mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’malemba amene ali m’nkhaniyo. Popeza ndife atumiki a Mulungu, tizionanso kuti tingagwiritse ntchito bwanji zimene taphunzirazo pothandiza ena. Komansotu kuti tipindule ndi zimene tikuphunzirazo, timafunika kusinkhasinkha.

Pamafunika Kukonzekeretsa Maganizo

Musanayambe kuphunzira, muyenera mumaonetsetsa kuti mwatenga Baibulo, buku limene mukufuna kuphunzira, cholembera komanso polembapo. Koma kodi mumakonzekeretsanso mtima wanu? Baibulo limanena kuti Ezara “anakonza mtima wake kuti aphunzire chilamulo cha Yehova ndi kuchichita ndiponso kuti aphunzitse mu Isiraeli malamulo ndi chilungamo.” (Ezara 7:10) Kodi munthu angachite bwanji zimenezi?

Pemphero limathandiza kuti tikhale ndi maganizo oyenera tikamaphunzira Mawu a Mulungu. Limathandizanso kuti zimene tikuphunzirazo zilowe komanso kukhazikika mumtima mwathu. Choncho musanayambe kuphunzira, muzipempha kaye Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyera. (Luka 11:13) Muzimupemphanso kuti akuthandizeni kumvetsa zimene mukuphunizirazo, kudziwa mmene zikugwirizanira ndi chifuniro chake komanso mmene zingakuthandizireni kudziwa zoyenera ndi zosayenera. Komanso muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni kuona mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuphunzirazo pa moyo wanu komanso mmene zingakuthandizireni kulimbitsa ubwenzi wanu ndi iye. (Miy. 9:10) Mukamaphunzira, ‘muzipempha kwa Mulungu’ kuti akupatseni nzeru. (Yak. 1:⁠5) Muzidzifufuza moona mtima ndipo mukaona kuti pali zina zimene mukufunika kusintha, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kusintha. Nthawi zonse ‘muziyamikira’ Yehova chifukwa cha zimene wakuthandizani kudziwa. (Sal. 147:⁠7) Kupemphera tisanayambe kuphunzira, kumathandiza kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. Izi zili choncho chifukwa timamvetsa zimene akutiuza kudzera m’Mawu ake komanso timaona mmene tingazigwiritsire ntchito pa moyo wathu.​—⁠Sal. 145:⁠18.

Tikamagwiritsa ntchito zimene tikuphunzira, timasiyana ndi anthu a m’dzikoli. Anthu ambiri amene si odzipereka kwa Mulungu amakonda kukayikira komanso kutsutsa zimene zinalembedwa m’Baibulo. Koma ife sitichita zimenezi chifukwa timakhulupirira Yehova. (Miy. 3:​5-7) Tikapanda kumvetsa mfundo inayake, sitiganiza kuti zimene tikuwerengazo ndi zolakwika. Tikafufuza koma osamvetsabe, timadikira kuti m’tsogolo, Yehova adzatithandiza kuzimvetsa. (Mika 7:⁠7) Monga mmene Ezara anachitira, timafunitsitsa kugwiritsa ntchito komanso kuphunzitsa ena zimene taphunzira. Maganizo amenewa amatithandiza kuti tizipindula ndi zimene tikuphunzira.

Mmene Tingaphunzirire

Musanayambe kuwerenga, onani mwachidule nkhani yonse imene mukufuna kuwerengayo. Mungachite izi poyamba n’kuganizira mozama mutu wa nkhaniyo. Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa zimene muti muphunzire m’nkhaniyo. Kenako onani mmene timitu ting’onoting’ono tikugwirizanira ndi mutu wa nkhaniyo. Mukatero, onani zithunzi, matchati komanso mabokosi amene ali m’nkhaniyo. Kenako dzifunseni kuti: ‘Malinga ndi zimene ndaonazi, kodi ndiphunzira chiyani m’nkhaniyi? Kodi indithandiza bwanji?’ Zimenezi zingakuthandezi kuti mumvetse zimene muti muphunzire.

Kenako mukhoza kuyamba kuwerenga. Nkhani zophunzira za mu Nsanja ya Olonda komanso m’mabuku ena, zimakhala ndi mafunso. Mukawerenga ndime, ndi bwino kudula mzere pansi pa yankho. Ngakhale zitakhala kuti nkhani imene mukuwerenga ilibe mafunso, mungachitebe bwino kudula mzere pansi pa mfundo zimene mukufuna muzizikumbukira kapena kuzigwiritsa ntchito. Ngati mwapeza mfundo yatsopano kwa inuyo, muzitherapo nthawi yokwanira kuti muimvetse. Muzionanso ngati pali zitsanzo komanso mfundo zimene zingakhale zothandiza mu utumiki kapena zimene mungadzazigwiritse ntchito pokamba nkhani m’tsogolo. Muziganiziranso anthu amene angalimbikitsidwe ngati mutawauza zimene mwaphunzirazo. Pomalizira penipeni, werenganinso mfundo zimene mwapeza m’nkhaniyo.

Muziwerenga malemba amene ali m’nkhaniyo ndipo muziona mmene akugwirizanira ndi mfundo yaikulu ya m’ndimeyo.

Muzidzifunsa kuti, mogwirizana ndi zimene ndaphunzirazi, ‘kodi ndi zinthu ziti zimene ndikufunika kusintha?’ Funso limeneli ndi lofunika kwambiri. Mukaphunzira mfundo inayake, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndaphunzirazi zikukhudza bwanji mmene ndimachitira zinthu komanso zolinga zanga? Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji zimene ndaphunzirazi kuti ndithetse vuto langa, ndisankhe bwino zinthu komanso kuti ndikwanitse zolinga zanga? Kodi ndingazigwiritse ntchito bwanji m’banja langa, mu utumiki komanso mu mpingo?’ Muziganiziranso mmene mungagwiritsire ntchito mfundozo, mutakumana ndi vuto linalake.

Mukamaliza kuphunzira mutu kapena nkhani, muzibwereramo kuti muone ngati mwaimvetsa bwino nkhaniyo. Onani ngati mukukumbukira mfundo zikuluzikulu komanso umboni wosonyeza kuti mfundo zimene zili m’nkhaniyo ndi zolondola. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzikumbukirabe zimene mwaphunzirazo ndipo mungathe kudzazigwiritsa ntchito m’tsogolo.

Zimene Tingaphunzire

Atumiki a Yehovafe tili ndi zinthu zambiri zimene tiyenera kuphunzira. Koma kodi tingayambire pati? Tsiku lililonse timayenera kukambirana lemba la tsiku ndi ndemanga yake kuchokera m’kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku. Mlungu uliwonse timapita kumisonkhano ya mpingo, ndipo timapindula kwambiri tikamakonzekera misonkhanoyi. Kuwonjezera pamenepa, ena amapeza nthawi yoti aziphunzira mabuku athu amene anatuluka iwowo asanaphunzire choonadi. Ena amasankha mavesi angapo pa kuwerenga Baibulo kwa mlunguwo n’kupeza nthawi yoti afufuze mavesiwo mozamirapo.

Koma kodi mungatani ngati mumakhala ndi nthawi yochepa moti simukwanitsa kukonzekera misonkhano yonse ya mlunguwo? Pewani kukonzekera mothamanga pongofuna kuti mumalize. Komanso si bwino kungosiyiratu osakonzekera chilichonse. M’malomwake, ganizirani zimene mungakwanitse kukonzekera mogwirizana ndi nthawi imene muli nayo. Ndiyeno zikonzekereni bwinobwino ndipo muzichita zimenezi mlungu uliwonse. Kenako, yesetsani kuwonjezera nthawi imene mumakonzekera kuti muzikonzekera nkhani zochulukirapo.

‘Mangani Banja Lanu’

Yehova amadziwa kuti amuna omwe ndi mitu ya mabanja ayenera kugwira ntchito mwakhama n’cholinga choti azisamalira banja lawo. Lemba la Miyambo 24:27 limanena kuti: “Konzekera ntchito yako yapanja, ndipo konza munda wako.” Koma kumbukirani kuti banja lanulo limafunikanso zinthu zauzimu. N’chifukwa chake lembali limanenanso kuti: “Ukatero ukamange banja lako.” Kodi amuna omwe ndi mitu ya mabanja angachite bwanji zimenezi? Lemba la Miyambo 24:3 limati: “Kuzindikira kumachititsa kuti [banja] lilimbe kwambiri.”

Kodi kuzindikira kungathandize bwanji kuti banja lanu lilimbe? Munthu wozindikira samangoona zinthu pamwambamwamba. Kuti muzitha kuphunzitsa bwino banja lanu, choyamba muyenera kulidziwa bwino banja lanulo. Muyenera kudziwa mmene munthu aliyense wa m’banja lanu akupitira patsogolo mwauzimu. Mukamakambirana muzimvetsera mwatcheru zimene akulankhula. Kodi amasonyeza kuti akudandaula kapena akwiya ndi zinazake? Kodi amakonda kwambiri zinthu zakuthupi? Mukamalalikira ndi ana anu, kodi amasonyeza kuti sachita manyazi anzawo akawazindikira kuti ndi a Mboni za Yehova? Kodi amasangalala mukamawerenga komanso kuphunzira nawo Baibulo? Kodi amayesetsa kutsatira malangizo a Yehova pa moyo wawo? Mafunso amenewa angakuthandizeni kuti mudziwe zoyenera kuchita n’cholinga choti banja lanu likhale lolimba mwauzimu komanso kuti aliyense m’banjamo azisonyeza makhalidwe abwino.

Phindu Limene Tingapeze

Kuphunzira Mawu a Mulungu patokha kumathandiza kuti tidziwe zinthu zambiri, komabe sitiyenera kuyamba kudzikuza chifukwa cha zimenezi. M’malomwake zimenezi ziyenera kutithandiza kukhala odzichipetsa. (Deut. 17:18-20) Mawu a Mulungu amatitetezanso ku “chinyengo champhamvu cha uchimo” chifukwa zimene taphunzira zikakhazikika mumtima mwathu, zimatithandiza kuti tikakumana ndi mayesero tisagonje. (Aheb. 2:1; 3:13; Akol. 3:5-10) Zimenezi zidzatithandiza kuti ‘tiziyenda mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna komanso kuti tizimukondweretsa pa chilichonse, pamene tikupitiriza kubala zipatso m’ntchito iliyonse yabwino.’ (Akol. 1:10) Tikamaphunzira Mawu a Mulungu, cholinga chathu chizikhala chimenechi ndipo tikachikwaniritsa, zinthu zimatiyendera bwino kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena