Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/14 tsamba 2
  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
km 6/14 tsamba 2

Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?

Masiku ano m’zipatala zambiri padziko lonse, muli madokotala amene amatha kupanga opaleshoni odwala popanda kuwaika magazi. Kodi mukudziwa bwino njira zimene madokotala angagwiritse ntchito popanda kumuika munthu magazi zimene mungasankhe? Muyenera kudziwa zimenezi kuti muzitha kusankha bwino chithandizo cha mankhwala kapena mtundu wa opaleshoni. Kuti mudziwe zambiri zokhudza nkhaniyi, werengani mofatsa mutu 7 m’buku lakuti Khalanibe M’chikondi cha Mulungu ndiponso malifalensi amene asonyezedwa m’nkhaniyi. Pambuyo pake, pempherani ndipo pogwiritsa ntchito mafunso amene ali m’ndime yotsatirayi, ganizirani zimene mwaphunzirapo.

(1) Kodi chifukwa chachikulu chimene a Mboni za Yehova amakanira kuikidwa magazi n’chiyani? (2) Pa nkhani ya chithandizo cha mankhwala, kodi a Mboni za Yehova amafuna chiyani? (3) Kodi odwala ali ndi ufulu wotani? (4) N’chifukwa chiyani ndi nzeru ndiponso ndi udindo wa munthu aliyense kusankha chithandizo cha mankhwala chosagwiritsa ntchito magazi? (5) Ngati munthu wataya magazi ambiri, kodi madokotala amathamangira kuchita zinthu ziwiri ziti? (6) Kodi muyenera kudziwa zinthu ziti zokhudza chithandizo cha mankhwala chosagwiritsa ntchito magazi? (7) Kodi n’zotheka kuchita maopaleshoni aakulu komanso ovuta popanda kuika munthu magazi? (8) Kodi pali kusintha kotani komwe kukuchitika m’zipatala zambiri?

Zithandizo zina zimene zasonyezedwa m’buku la Chikondi cha Mulungu komanso malifalensi omwe ali m’ndime yomaliza ino n’zoti munthu aliyense asankhe payekha mogwirizana ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo. Kodi mwasankha kale chithandizo chamankhwala chimene mungathe kulandira ndiponso chimene mungalole kuti ana anu apatsidwe? Nanga mwalemba zomwe mwasankhazo pa Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala (DPA)? Kuti mudziwe zambiri pa nkhani imeneyi, werengani mofatsa “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” a mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, ndiponso ya October 15, 2000. Kenako gwiritsani ntchito zimene zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006, pamutu wakuti, “Kodi Ndimaiona Bwanji Nkhani Yokhudza Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zachipatala Zogwiritsa Ntchito Magazi Anga Omwe?” posankha zimene mukuvomereza kapena kukana. Pomaliza, onetsetsani kuti mwalemba bwinobwino zimene mwasankhazo pakhadi lanu la DPA. Anthu omwe mwawasankha kukuimirani ndiponso achibale anu omwe si Mboni ayenera kudziwa bwino zimene mwasankhazo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena