Ndandanda ya Mlungu wa August 25
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 25
Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 15 ndime 7-12 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 14-16 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zitsanzo za Zomwe Zinachitika.Pemphani wofalitsa mmodzi kapena awiri kuti achite chitsanzo chosonyeza zomwe zinachitikadi pamene ankauza ena za Ufumu molimba mtima. Kambiranani mwachidule lemba la Aheberi 6:11, 12, ndipo kenako tsindikani chifukwa chake tiyenera kuchita khama tikamalalikira za Ufumu wa Mulungu.
Mph. 10: Kuuza Ena za Ufumu—Gawo 1. Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 280, ndime 1 mpaka 4.
Mph. 15: Kuuza Ena za Ufumu—Gawo 2. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 280 ndime 5 mpaka tsamba 281 ndime 1. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuthandiza munthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni.
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero