Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira August 25, 2014.
Kodi lemba la Levitiko 18:3 lingatithandize bwanji kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya zabwino ndi zoipa? (Aef. 4:17-19) [July 7, w02 2/1 tsa. 29 ndime 4]
Kodi lamulo la pa Levitiko 19:2 likutiphunzitsa chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kulitsatira? [July 7, w09 7/1 tsa. 9 ndime 5]
Kodi tingaphunzire chiyani pa lamulo limene Mulungu anapatsa Aisiraeli loti pokolola azisiya zinthu zina m’munda kuti anthu ena azikunkha? (Lev. 19:9, 10) [July 7, w06 6/15 tsa. 22-23 ndime 13]
N’chifukwa chiyani tinganene kuti lamulo loti “diso kulipira diso” silinkalimbikitsa kuti munthu akalakwiridwa azibwezera? (Lev. 24:19, 20) [July 14, w09 9/1 tsa. 22 ndime 3-4]
Kodi ndi pa zochitika zotani pamene Aisiraeli ankaloledwa kulandira chiwongoladzanja pa ndalama zomwe akongoza munthu, nanga ndi pazochitika zotani pomwe sankaloledwa? (Lev. 25:35-37) [July 21, w04 5/15 tsa. 24 ndime 3]
N’chifukwa chiyani Baibulo limangotchula mafuko 12 a Isiraeli pamene analipo mafuko 13? (Num. 1:49, 50) [July 28, w08 7/1 tsa. 21]
Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene ankachitira Alevi achikulire, zomwe zalembedwa pa Numeri 8:25, 26? [Aug. 11, w04 8/1 tsa. 25 ndime 1]
N’chifukwa chiyani Aisiraeli anayamba kung’ung’udza ngakhale kuti Yehova anawachitira zozizwitsa zambiri pa ulendo wawo wochoka ku Iguputo? Nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani? (Num. 11:4-6) [Aug. 18, w95 3/1 tsa. 15-16 ndime 10]
Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mose anayankha atamva kuti Eledadi ndi Medadi akuchita zinthu ngati aneneri? (Num. 11:27-29) [Aug. 18, w04 8/1 tsa. 26 ndime 4]
Kodi tikuphunzira chiyani pa lamulo limene Aisiraeli anapatsidwa loti “azisokerera mphonje m’mphepete mwa zovala zawo”? (Num. 15:37-39) [Aug. 25, w04 8/1 tsa. 26 ndime 7]