Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Pali zinthu zambiri zimene zikuchitika m’dziko lathu lino. Panopa tili ndi mipingo yokwana 1,417 komanso ofalitsa 92,000. Tilinso ndi akulu okwana 6,491 ndi atumiki othandiza 5,707. Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kutidalitsa kuti pakhale abale oyenera oti azithandiza m’mipingo yathu.