Ndandanda ya Mlungu wa June 8
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 8
Nyimbo Na. 18 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 14 ndime 1-9 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Samueli 19-21 (8 min.)
Na. 1: 2 Samueli 19:24-37 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Kodi Mungatani Kuti Muzikhala Osangalala?—igw tsa. 22 ndime 1-3 (5 min.)
Na. 3: Khalani ndi Mbiri Yabwino Ngati Timoteyo?—bt tsa. 122-123 ndime 13-17 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Kumbukirani masiku akale”—Deut. 32:7.
10 min: “Kumbukirani Masiku Akale.” Nkhani yochokera pa mutu wa mwezi uno. Werengani ndi kukambirana lemba la Deuteronomo 4:9 ndi 32:7 komanso Salimo 71:15-18. Kenako fotokozani zimene tingapindule ngati tikukumbukira anthu komanso zinthu zakale zokhudza gulu lathu. Limbikitsani omverawo kuti nthawi zina azikambirana nkhani za mutu wakuti “Kale Lathu” zimene zimapezeka mu Nsanja ya Olonda yophunzira pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. Fotokozani mwachidule nkhani zina zomwe zili mu Msonkhano wa Utumiki wa mwezi uno komanso kambiranani kugwirizana kwake ndi mutu wa mwezi uno.
20 min: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kuyambitsa Phunziro Lachidule Pogwiritsa Ntchito Kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu.” Nkhani yokambirana yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Tchulani chiwerengero cha maulendo obwereza omwe abale ndi alongo anapanga chaka cha utumiki chapitachi, zomwe zikusonyeza kuti akhoza kukhala ndi maphunziro ambiri. Kenako chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa waluso akuyambitsa phunziro la Baibulo lachidule pogwiritsa ntchito chitsanzo chimene chikupezeka m’bokosi lakuti “Zimene Munganene Mukamayambitsa Phunziro la Baibulo Lachidule” lomwe lili kumanzereku. Limbikitsani onse kuti aziyambitsa phunziro la Baibulo lachidule.
Nyimbo Na. 29 ndi Pemphero