Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda June 1
“Tikucheza ndi anthu a m’dera lino ndipo tikukambirana nawo kufunika kwa Baibulo. Ambiri amaona kuti sayansi ikupangitsa anthu kumaona kuti Baibulo si lolondola. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi mukuona kuti tiyenera kukhulupirira Baibulo? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani chitsanzo chimodzi chosonyeza kuti Baibulo ndi lolondola. [Werengani Yobu 26:7.] Magaziniyi ikufotokoza kugwirizana kwa zimene Baibulo limanena ndi zimene asayansi apeza.”
Galamukani! June
“Popeza masiku ano anthu ambiri akuvutika ndi matenda, tikukambirana ndi anthu vesi lolimbikitsa la m’Baibulo ili. [Werengani Yesaya 33:24a.] Kodi mukuganiza kuti moyo wathu ukanakhala wotani tikanakhala kuti sitidwala? [Yembekezerani ayankhe.] Posachedwapa ulosi umenewu ukwaniritsidwa. Komabe magaziniyi ikufotokoza mfundo 5 zomwe zingatithandize kuti tikhale ndi moyo wathanzi panopa.”