Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda August 1
“Tikucheza ndi anthu mwachidule n’kumakambirana nawo za vuto lomwe limagwera tonsefe. Inu mungandivomereze kuti munthu amene tinkamukonda akamwalira, zimakhala zowawa kwambiri. Koma taonani mawu olimbikitsa awa ochokera m’Baibulo. [Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Baibulo limatithandiza kukhala ndi chiyembekezo choti abale athu amene anamwalira adzaukitsidwa. Magazini iyi ikufotokoza mmene zimenezi zidzachitikire.”
Galamukani! August
“Tikufuna kukusonyezani nkhani imene ikunena za kuchuluka kwa zinthu zomwe zimapezeka m’maselo a anthufe. [Asonyezeni chikuto cha Galamukani! ya August.] Anthu ena amakhulupirira kuti zinthu zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, pomwe ena amaona kuti pali winawake amene analenga zamoyo. Nanga inuyo maganizo anu ndi otani? [Yembekezerani ayankhe.] Magaziniyi ikufotokoza zomwe akatswiri apeza, zomwe zikusonyeza kuti maselo anapangidwa mogometsa. Zimenezi zachititsa asayansi ena kuyamba kuganiza kuti pali winawake amene analenga zinthu zamoyo.”