Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Abale awiri oimira likulu la Mboni za Yehova anachezera nthambi yathu kuyambira pa 4 February mpaka pa 10 February, 2015. Lamlungu pa 8 February, panali msonkhano womwe unachitikira pa Malo a Misonkhano a Lilongwe. Anthu enanso m’dziko lathu lino anamvetsera msonkhanowu kudzera pa foni ndi pa Intaneti m’malo okwana 6. Anthu onse amene anamvetsera msonkhanowu analipo okwana 43,479. Misonkhano yotereyi imakhala yolimbikitsa kwambiri. Tikukhulupirira kuti pa msonkhano wangati womwewu m’tsogolomu, tidzatha kulumikiza m’malo oposa 6.