Ndandanda ya Mlungu wa August 10
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 10
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 17 ndime 1-8 ndi chigawo chachitatu patsamba 168 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 21-22 (8 min.)
Na. 1: 1 Mafumu 22:13-23 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Kodi Mungatani Kuti Mukhale pa Ubwenzi ndi Mulungu?—igw tsa. 28 ndime 1-4 (5 min.)
Na. 3: Mavuto Amene Angabwere Chifukwa Chokonda Ndalama—lv tsa. 176-179 ndime 14-16 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.”—Yos. 24:15.
10 min: “Ine ndi a M’nyumba Yanga, Tizitumikira Yehova.” Nkhani yochokera pa mutu wa mwezi uno. Werengani Deuteronomo 6:6, 7; Yoswa 24:15 ndi Miyambo 22:6 ndipo kenako kambiranani kuti tingatsatire bwanji malangizo a m’malemba amenewa. Tsindikani mfundo yakuti amuna ayenera kutsogolera mabanja awo pa zinthu zauzimu. Tchulani zinthu zosiyanasiyana zomwe gulu latulutsa zomwe ndi zothandiza mabanja. Fotokozaninso mwachidule nkhani zina za m’Msonkhano wa Utumiki zomwe tiphunzire mwezi uno. Mufotokozenso mmene nkhanizo zikugwirizanirana ndi mutu wa mwezi uno.
20 min: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muziphunzitsa Ofalitsa Atsopano.” Nkhani yokambirana. Funsani omvera kuti afotokoze mmene makolo angagwiritsire ntchito mfundo za m’nkhaniyi pothandiza ana awo kuti akule mwauzimu. Chitani chitsanzo cha bambo akukonzekera ulaliki ndi mwana wake wamwamuna kapena wamkazi.
Nyimbo Na. 93 ndi Pemphero