Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda January 1
“Anthu ambiri amaona kuti nthawi zonse m’boma mumachitika zachinyengo. Koma kodi n’chiyani chimachititsa zimenezi? [Yembekezerani ayankhe.] Lemba ili likutithandiza kudziwa chifukwa chake. [Werengani Mlaliki 7:20.] Magaziniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena, zomwe zidzathandize kuti chinyengo chithe. Ngati mungakonde ndingakupatseni kuti mukaiwerenge.”
Galamukani! January
“Asayansi ena amakhulupirira kuti zinthu zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Koma ena sakhulupirira zimenezi. Kodi inuyo mukuganiza kuti moyo unayamba bwanji? [Yembekezerani ayankhe.] Asayansi atafufuza kwa zaka zambiri, akuona kuti payenera kuti pali winawake amene analenga zamoyo. Zimenezitu zikugwirizana ndi zomwe Baibulo limanena. [Werengani Salimo 36:9.] Magaziniyi ikufotokoza chifukwa chake anthu ambiri amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa.”