Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira June 29, 2015.
Kodi chinalakwika n’chiyani ndi mawu amene Mikala anauza Davide, nanga anthu okwatirana angaphunzirepo chiyani? (2 Sam. 6:20-23) [May 11, w11 8/1 tsa. 12 ndime 1]
Kodi mneneri Natani anatani Yehova atamudzudzula chifukwa cholimbikitsa Davide kuti apitirize mapulani ake omanga kachisi? (2 Sam. 7: 2, 3) [May 11, w12 2/15 tsa. 24 ndime 6-7]
N’chifukwa chiyani Natani anauza Davide fanizo la pa 2 Samueli 12:1-7, m’malo mongomuuza kuti wachita tchimo lalikulu? Nanga zimenezi zingatithandize bwanji kuti tiziphunzitsa mogwira mtima? [May 18, w12 2/15 tsa. 24 ndime 2-3]
N’chifukwa chiyani Aisiraeli anakopeka mosavuta ndi Abisalomu, nanga ifeyo tingatani kuti tisakopeke ndi anthu amtima ngati wa Abisalomu? (2 Sam. 15:6) [May 25, w12 7/15 tsa. 13 ndime 7]
Kodi Yehova anasamalira bwanji Davide pa nthawi yovuta, nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani? (2 Sam. 17:27-29) [June 1, w08 9/15 tsa. 6 ndime 15-16]
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Davide anachitira Itai, yemwe sanali Mwisiraeli? (2 Sam. 18:2) [June 1, w09 5/15 tsa. 27 ndime 7]
Kodi Akhristu achikulire angaphunzire chiyani kwa Barizilai? (2 Sam. 19:33-35) [June 8, w07 7/15 tsa. 15 ndime 1-2]
Kodi mawu amene Davide ananena angalimbikitse bwanji atumiki a Yehova okhulupirika masiku ano? (2 Sam. 22:26) [June 15, w10 6/1 tsa. 26 ndime 6-7
odi Natani anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika kwa Yehova, nanga ifeyo tingamutsanzire bwanji? (1 Maf. 1:11-14) [June 22, w12 2/15 tsa. 25 ndime 1, 4-5]
Kodi ndi pa nkhani ziti pamene Mkhristu angayambe kudzikhululukira chifukwa chosatsatira malamulo a Mulungu, ngati mmene Solomo anachitira? (1 Maf. 3:1) [June 29, w11 12/15 tsa. 10 ndime 12-14]