Ndandanda ya Mlungu wa June 22
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 22
Nyimbo Na. 109 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 14 ndime 16-20 ndi bokosi patsamba 147 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 1-2 (8 min.)
Na. 1: 1 Mafumu 1:15-27 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Amakhala Osangalala?—igw tsa. 23 ndime 1-3 (5 min.)
Na. 3: Zimene Mungachite Kuti Yehova Akudalitseni mu Utumiki—bt tsa. 126-127 ndime 5-8 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Kumbukirani masiku akale”—Deut. 32:7.
15 min: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mlembi. Fotokozani zimene abale ndi alongo anachita pa nyengo ya Chikumbutso ndipo ayamikireni chifukwa cha zimene anachita. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo pamene ankagawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso.
15 min: Kodi Yehova Anakugwirani Bwanji Dzanja? (Yes. 41:13) Funsani munthu mmodzi kapena awiri amene akhala akutumikira mokhulupirika kwa nthawi yaitali. Kodi Yehova amawathandiza bwanji kupirira mavuto amene akukumana nawo pamene akumutumikira.
Nyimbo Na. 107 ndi Pemphero