Tiziphunzira kwa Ofalitsa Aluso
Kunena zoona, timasangalala kwambiri kukhala ndi ofalitsa aluso mumpingo. Ena mwa ofalitsa amenewa akhala akutumikira Yehova kwa zaka zambiri ndipo ali ndi luso pomwe ena angopeza kumene luso limeneli. Ofalitsa alusowa aona mmene Yesu wakhala akutsogolera mpingo m’masiku otsiriza ano. Aona mmene ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale otsatira a Yesu yakhala ikuyendera bwino. (Mat. 28:19, 20) Pogwira ntchitoyi, ofalitsawa akhala akulandira “mphamvu yoposa yachibadwa” yomwe yawathandiza kuti azipirira mavuto komanso mayesero. (2 Akor. 4:7) Choncho tikhoza kuphunzira zambiri kwa ofalitsa amenewa. Nawonso amasangalala kuphunzitsako ena zimene aphunzira. (Sal. 71:18) Ndiyetu tiyeni tiziyesetsa kuphunzira kwa ofalitsa alusowa. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?
Mu Utumiki. Kuti ofalitsa atsopano kapena amene sakudziwa zambiri akhale ndi luso pa ntchito yolalikira, ayenera kuphunzitsidwa. Munthu akhoza kuphunzira zinthu zambiri akamaona wofalitsa waluso akulalikira. (Onani nkhani ya mutu wakuti “Kodi Tingatani Kuti Tizikondabe Kulalikira?” mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2015 ndime yachitatu pansi pa kamutu kakuti “Tizithandiza Atsopano.”) Kodi inuyo mwapindula bwanji chifukwa cholalikira pamodzi ndi ofalitsa aluso?
Kodi mungapemphe wofalitsa waluso kuti mudzapite naye kokalalikira? Ngati wofalitsa walusoyo ndi wachikulire ndipo amadwaladwala, kodi mungakonze zoti muzitenga wophunzira Baibulo wanu kuti muzikaphunzirira kunyumba kwake? Mukamaliza kuphunzira muzipempha wofalitsa walusoyo kuti akufotokozereni zinthu zimene muyenera kusintha komanso mungamupemphe kuti akupatseni malangizo omwe angakuthandizeni kuti muzilalikira mwaluso.
Muzipeza Nthawi Yocheza Nawo: Kuti mudziwane ndi ofalitsa aluso muyenera kucheza nawo. Mungaitane ofalitsawo kuti mudzachitire nawo limodzi kulambira kwa pabanja ndipo muziwafunsa mafunso. Ngati wofalitsayo ndi wachikulire komanso amadwaladwala, mungakonze zoti mukachitire kulambira kwa pabanjako kunyumba kwake. Mungamufunse mafunso ngati awa: Kodi anaphunzira bwanji Baibulo? Kodi wapeza madalitso otani? Kodi zinthu zasintha bwanji kuchokera nthawi imene anaphunzira choonadi? Nanga kutumikira Yehova kwamuthandiza bwanji kukhala wosangalala?
Dziwani kuti nawonso ofalitsa aluso angalephere kuchita zinthu zina bwinobwino. Choncho musamayembekezere zambiri. Mofanana ndi tonsefe, anthu amene akhala akugwira ntchito yolalikira kwa nthawi yaitali ali ndi mphatso zosiyanasiyana. (Aroma 12:6-8) Ena mwa ofalitsawa ndi achikulire kwambiri ndipo sachitanso zambiri ngati kale. Komabe tikhoza kuphunzira zambiri kwa ofalitsawa chifukwa akudziwa zambiri komanso akhala akutumikira Yehova mokhulupirika.