Amenewanso Muziwaganizira
M’mipingo yambiri muli ofalitsa amene sangathe kuchita zambiri mu utumiki chifukwa cha matenda kapena ukalamba. (2 Akor. 4:16) Ndiye kodi mungapempheko ofalitsa amenewa kuti azikhala nanu mukamachititsa phunziro la Baibulo? Ngati wofalitsayo ali woti sangathe kuchoka pakhomo, mwina mungachite bwino kupita ndi wophunzira wanu kunyumba kwa wofalitsayo n’kukaphunzirira komweko. Komanso nthawi zina mungatenge wofalitsa yemwe amalephera kuchita zambiri mu utumiki chifukwa cha matenda kuti mukalalikire naye limodzi khomo ndi khomo nyumba zochepa kapena kupita naye ku ulendo wobwereza. Mungapite naye kwa munthu mmodzi kapena awiri. Ofalitsa achikulire ambiri amakhala aluso mu utumiki, choncho kuchita zimenezi sikungowaganizira iwowo, koma inunso mudzapindula kwambiri. (Aroma 1:12) Kuwonjezera pamenepo, mukamayesetsa kusonyeza chikondi kwa ena m’njira imeneyi, Yehova adzakudalitsani.—Miy. 19:17; 1 Yoh. 3:17, 18.