Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/15 tsamba 4
  • Ntchito Yoitanira Anthu ku Msonkhano Wachigawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Yoitanira Anthu ku Msonkhano Wachigawo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Msonkhano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Ntchito Imene Imakhala ndi Zotsatira Zabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Ntchito Yoitanira Anthu Kumsonkhano Wachigawo
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa April 2
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
km 6/15 tsamba 4

Ntchito Yoitanira Anthu ku Msonkhano Wachigawo

1. Kodi ntchito yoitanira anthu kumsonkhano wachigawo idzayamba liti?

1 Ngati mwakonza chakudya chapadera komanso chodula, ndipo mukufuna kuti anthu a m’banja lanu komanso anzanu adye chakudyacho, n’zodziwikiratu kuti mungawaitane mwansangala n’cholinga choti asalephere kudzadya. N’chimodzimodzinso ndi msonkhano wachigawo wa chaka chino. Pali zambiri zimene zachitika pokonzekera phwando lauzimu limeneli. Kutatsala milungu itatu kuti msonkhano wanu uyambe, mudzakhala ndi mwayi wogwira ntchito yoitanira anthu kumsonkhanowu. Kodi tingatani kuti tidzaitanire anthu kumsonkhanowu mwansangala, n’cholinga choti asadzalephere kubwera?

2. Kodi tiyenera kuganizira mfundo ziti, zomwe zidzatithandize kuti tidzagwire mwakhama ntchito yoitanira anthu kumsonkhano?

2 Kuti tione kufunika kogwira ntchito imeneyi mwakhama, tiyenera kuganizira mmene chakudya chauzimu chimene Yehova amatipatsa pamisonkhano yachigawo chimatithandizira. (Yes. 65:13, 14) Tisaiwalenso kuti ntchito yoitanira anthu kumsonkhano, yomwe imachitika chaka chilichonse, imakhala ndi zotsatira zabwino. (Onani bokosi lakuti, “Ena Omwe Timawaitana Amabwera.”) Anthu ena amene tidzawaitanire kumsonkhawu, adzabweradi. Komabe ngakhale zitakhala kuti anthu ambiri sadzabwera, tikadzagwira ntchitoyi, zidzachititsa kuti Yehova alemekezeke komanso zidzasonyeza kuti iye ndi wowolowa manja.—Sal. 145:3, 7; Chiv. 22:17.

3. Kodi tizidzagawira bwanji timapepala toitanira anthu kumsonkhano?

3 Bungwe la akulu lililonse liyenera kuona njira yabwino imene mpingo wawo ungatsatire pogawira timapepalati. Angaonenso ngati pakufunika kuti ofalitsa azisiya kapepala pakhomo lomwe sanapezepo anthu kapena azipereka kapepalaka kwa anthu, m’malo opezeka anthu ambiri m’gawo lawo. Kumapeto kwa mlungu tingagawire kapepalaka limodzi ndi magazini, ngati tapeza anthu achidwi. Ntchito yogawira timapepalati ikadzatha, tidzasangalala kwambiri podziwa kuti tagwira nawo mwakhama ntchitoyi ndipo tayesetsa kuitanira anthu ambiri kuphwando lauzimu lomwe Yehova wakonza.

Zimene Munganene.

Mukapereka moni, munganene kuti: “Tikukuitanirani kumsonkhano wofunika kwambiri womwe udzachitike padziko lonse. Tsiku, nthawi komanso malo omwe kudzachitikire msonkhanowu kudera lathu lino, talemba pakapepala pomwepa.”

Ena Omwe Timawaitana Amabwera

  • Zaka zingapo zapitazo, mlongo wina anagwira nawo ntchito yoitanira anthu kumsonkhano. Koma ankadzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amene tikuwaitanawa adzabweradi pamsonkhanowu kapena tikungodzivutitsa?’ Koma Loweruka m’mawa msonkhanowu utayamba, anaona kuti pafupi ndi iyeyo panali bambo wina wa chipembedzo chachisiki. Kenako anaganiza zocheza naye kuti amudziwe. Bamboyu anafotokoza kuti anabwera kumsonkhanowu chifukwa analandira kapepala. Anafunsanso mafunso angapo ndipo mlongoyo anamuyankha. Ananena kuti anasangalala ndi nkhani zomwe zinakambidwa pamsonkhanowo. Komanso anachita chidwi kwambiri ndi mmene anthu anavalira komanso khalidwe lawo. Masana a tsiku lomweli mlongoyu anachezanso ndi banja lina lomwe linakhala moyandikana naye. Nawonso anabwera kumsonkhanowu chifukwa analandira kapepala kowaitana. Anasangalala kwambiri ndi msonkhanowo moti ananena kuti abweranso tsiku lotsatira. Mlongoyo anazindikira kuti ntchito yoitanira anthu kumsonkhano ndi yofunika kwambiri.

  • Pamsonkhano wina waposachedwapa, m’bale ndi mlongo wina omwe ndi apainiya, anacheza ndi banja lina lachikulire. Banjalo linawauza kuti kanali koyamba kufika pamsonkhanowo. Apainiyawo atawafunsa amene anawaitana, anayankha kuti: “Tsiku lina titafika kunyumba tinapeza kapepala kotiitanira kumsonkhanowu kali pakhomo.” Banjali linati linawerenga kapepalako komanso linalemba kuseri kwake popempha munthu woti aziphunzira nawo Baibulo. Linapemphanso kuti awatumizire kabuku komwe kanasonyezedwa pakapepalako. Pa nthawi yopuma, anthu ena pamsonkhanopo anadya ndi banjali chakudya chimene anabweretsa. Banjali linasangalala kwambiri ndi zimene anamva tsikulo moti ananena kuti abweranso tsiku lotsatira. Panakonzedwa zoti munthu wina adzawayendere komanso kuyamba kuphunzira nawo Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena