Ndandanda ya Mlungu wa June 29
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 29
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 15 ndime 1-10 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 3-6 (8 min.)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (20 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Kumbukirani masiku akale”—Deut. 32:7.
15 min: Mabuku Ogawira mu July. Nkhani yokambirana. Kambiranani mfundo zimene zikupezeka m’mabuku amene tidzagawire mwezi umenewu. Kenako chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuthandiza munthu watsopano mmene angagawirire mabukuwo.
15 min: Muzigwiritsa Ntchito Buku Lapachaka la 2015. Nkhani yokambirana. Kambiranani mwachidule “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.” Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zochititsa chidwi palipoti la padziko lonse. Pomaliza, limbikitsani anthu onse kuti ayesetse kuwerenga Buku Lapachaka mpaka kulimaliza.
Nyimbo Na. 108 ndi Pemphero