Ndandanda ya Mlungu wa October 19
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 19
Nyimbo Na. 80 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 20 ndime 8-15 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mbiri 8-11 (8 min.)
Na. 1: 1 Mbiri 11:15-25 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Pemphero Limathandiza Kwambiri—bh tsa. 170-173 ndime 16-20 (5 min.)
Na. 3: Kodi Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?—bh tsa. 218-219 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Khalani “ozikika mozama” ndiponso ‘okhazikika m’chikhulupiriro.’—Akol. 2:6, 7.
20 min: “Kodi Tingatani Kuti Tiziwafika pa Mtima Anthu Amene Timaphunzira Nawo?” Mafunso ndi mayankho. Chitani zitsanzo ziwiri. M’chitsanzo choyamba, mwininyumba akunena kuti mwana wake anamwalira ndipo ali kumwamba. Ndiyeno wofalitsa akuwerenga lemba la Mlaliki 9:5 pofotokoza zimene zimachitika munthu akamwalira. Koma vesili silinamuthandize kwenikweni mwininyumbayo ndipo akutsutsa zimene wofalitsayo akufotokoza. M’chitsanzo chachiwiri, wofalitsayo akulankhula mwaluso kwambiri pofotokozera mwininyumbayo zakuti akufa adzauka ndipo akuwerenga naye lemba la Yohane 5:28, 29. Mwininyumbayo akuoneka kuti walimbikitsidwa kwambiri ndi lembali ndipo akumvetsera pamene wofalitsayo akulankhula.
10 min: Kaya Ndinu Wamkulu Kapena Mwana, Mukhoza Kukhala Chitsanzo Kwa Ena. (Afil. 3:17; 1 Tim. 4:12) Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2015, tsamba 71 ndime 2 mpaka 72 ndime 5 komanso tsamba 76 ndi 77. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Nyimbo Na. 90 ndi Pemphero