Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Timasangalala tikamalalikira uthenga wabwino, koma chomwe chimatisangalatsa kwambiri ndikupeza munthu woti tiziphunzira naye Baibulo. Ndife okondwa kukudziwitsani kuti mwezi wa April tinachititsa maphunziro a Baibulo okwana 96,057 komanso tinagawira mabuku 49,337. Ziwerengero zimenezi zikuposa zina zonse za m’mbuyomu ndipotu umenewu ndi umboni woti Yehova akudalitsa ntchito yathu pamene tikumvera lamulo la Yesu lopezeka pa Mateyu 28:19, 20. Zimenezi zikusonyezanso kuti pali ntchito yambiri yoti tigwire. Choncho tikupempha wofalitsa aliyense kuti apitirize kuthandiza anthu kudziwa Mulungu kuti ayambe kuyenda panjira yopita ku moyo wosatha.