Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda November 1
“Magulu awiri akayamba kumenyana, mbali iliyonse imaganiza kuti Mulungu akuwathandiza. Koma kodi Mulungu amavomereza zoti anthu azimenya nkhondo? [Yembekezerani ayankhe.] Magaziniyi ikufotokoza chifukwa chake Mulungu ankamenya nkhondo kale. Ikufotokozanso zimene adzachite posachedwapa, zomwe zidzathetseretu nkhondo padzikoli.” Werengani Salimo 46:9 ndipo kenako apatseni magaziniwo.
Galamukani! November
“Anthu ambiri padzikoli amakhumudwa chifukwa cha chinyengo komanso zinthu zabodza zomwe zipembedzo zosiyanasiyana zimaphunzitsa. Kodi mukuganiza kuti zipembedzo zili ndi tsogolo lotani? [Yembekezerani ayankhe.] Magaziniyi ikufotokoza ulosi wochititsa chidwi wa m’buku la Chivumbulutso umene unaneneratu kuti m’nthawi yathu ino anthu ambiri adzatuluka m’chipembedzo chonyenga. Ulosiwu umasonyezanso kuti posachedwapa zipembedzo zonse zonyenga ziwonongedwa.”