Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 December tsamba 3
  • “Tiyeni Tipite Kukakwera Phiri la Yehova”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Tiyeni Tipite Kukakwera Phiri la Yehova”
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Mtendere—Zenizenizo
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mtendere wa Dziko Lonse—Motani Ndipo Liti?
    Galamukani!—1987
  • Mmene Dziko Lidzagwirizanitsidwira
    Galamukani!—1994
  • Kutheratu kwa Chiwawa—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 December tsamba 3

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 1-5

“Tiyeni Tipite Kukakwera Phiri la Yehova”

2:2, 3

“M’masiku otsiriza”

Nthawi yathu ino

“Phiri la nyumba ya Yehova”

Kulambira Yehova movomerezeka

“Mitundu yonse idzakhamukira kumeneko”

Anthu olambira Mulungu movomerezeka amakhala gulu limodzi logwirizana

“Bwerani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova”

Olambira oona amaitana anthu ena kuti azilambira nawo limodzi

“Iye akatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo”

Yehova amatiphunzitsa ndiponso kutithandiza kuyenda m’njira zake pogwiritsa ntchito Mawu ake

Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana akupita kuphiri la Yehova

2:4

“Anthuwo sadzaphunziranso nkhondo”

Yesaya anafotokoza kuti anthu adzasula zida zankhondo kuti zikhale zolimira pofuna kusonyeza kuti anthu a Yehova azidzakhala mwamtendere. Kodi zida zimenezi zinali zotani?

‘Malupanga akhale makasu a pulawo’

1 Khasu la pulawo ndi limene linkagalauza nthaka ndipo nthawi zina linkakhala lachitsulo.—1 Sam. 13:20

‘Mikondo ikhale zida zosadzira mitengo’

2 Chida chosadzira mitengo chinali chooneka ngati chikwakwa. Ankagwiritsanso ntchito chidachi posadza mpesa.—Yes. 18:5

Lupanga ndi mkondo
Khasu la pulawo ndi chosadzira mitengo
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena