Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 February tsamba 6
  • Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Pitirizani Kulimbitsa Chiyembekezo Chanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Yembekezani Yehova Kuti Mukhale Olimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Chiyembekezo Chodalirika Mungachipeze Kuti?
    Galamukani!—2004
  • Tili ndi Chiyembekezo Chomwe Sichitikhumudwitsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 February tsamba 6
Banja likuyeserera zokanena muutumiki pa Kulambira Kwa pa Banja

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu

Chiyembekezo chili ngati nangula amene amathandiza kuti sitima isasunthe. (Aheb. 6:19) Zili choncho chifukwa chimatithandiza kuti tisasokonezeke mwauzimu tikakumana ndi mavuto aakulu okhala ngati mafunde oopsa. (1 Tim. 1:18, 19) Mavutowa akhoza kukhala matenda aakulu, mavuto azachuma, imfa ya munthu amene tinkamukonda kapena mayesero ena alionse.

Chikhulupiriro komanso chiyembekezo chimatithandiza kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono zimene Mulungu watilonjeza. (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 11:13, 26, 27) Choncho kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, tiyenera kumaganizira kwambiri zimene Mulungu walonjeza m’Mawu ake. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhalabe osangalala pamene takumana ndi mayesero.​—1 Pet. 1:6, 7.

ONERANI VIDIYO YAKUTI TIZISANGALALA NDI CHIYEMBEKEZO CHATHU. KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • N’chifukwa chiyani Mose ndi chitsanzo chabwino?

  • Kodi amuna okwatira ali ndi udindo wotani m’banja?

  • Kodi ndi nkhani ziti zimene mungakambirane pa Kulambira kwa Pabanja?

  • Kodi kukhala ndi chiyembekezo kungakuthandizeni bwanji kuti musataye mtima mukakumana ndi mayesero?

  • Kodi inuyo mukuyembekezera zinthu ziti?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena