Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya February 2017
FEBRUARY 6-12
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 47-51
it 1-E 643 ¶4-5
Kuthetsa Ukwati
Kutha kwa Ukwati Kophiphiritsa. Nthawi zina Malemba amagwiritsira ntchito mawu akuti ukwati mophiphiritsa. (Yes. 54:1, 5, 6; 62:1-6) N’chimodzimodzinso ndi mawu akuti kuthetsa ukwati, nawonso amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa.—Yer. 3:8.
Mu 607 B.C.E., ufumu wa Yuda unagonjetsedwa ndipo Yerusalemu anawonongedwa. Kenako anthu a mumzindawo anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Zaka zingapo m’mbuyomo Yehova anali atafunsa Ayuda omwe adzapite ku ukapolo kuti: “Chili kuti chikalata chothetsera ukwati wa mayi wanu yemwe ndinamuthamangitsa?” (Yes. 50:1) “Mayi” awo, kapena kuti mtundu wawo, anali atathamangitsidwa pa chifukwa chomveka. Sikuti Yehova anangofuna kuphwanya pangano kapena kungothetsa ukwatiwo, koma chinali chifukwa choti anthuwo anakana kutsatira pangano la Chilamulo. Koma Aisiraeli otsala analapa ndipo anapempha Yehova kuti akhalenso mwamuna wawo. M’chaka cha 537 B.C.E., patatha zaka 70 dziko la Yuda lili bwinja, Yehova anabwezeretsa anthu ake m’dziko lawo monga mmene analonjezera. Iye anachita izi chifukwa cha dzina lake.—Sal. 137:1-9.