Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya March 2017
MARCH 13-19
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 5-7
Yeremiya Yemwe Anali Mneneri Wosadziwika Anapereka Uthenga wa Ziweruzo za Mulungu
7 Yehova anachenjeza kuti, “Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzapambana.” (Yeremiya 1:19) Kodi n’chifukwa chiyani Ayuda ndi atsogoleri awo ankafuna kumenyana ndi mneneriyu? Chinali chifukwa chakuti uthenga wake unkadzudzula zoipa zimene iwo ankachita komanso njira zimene ankagwiritsa ntchito polambira. Yeremiya sanafooke ndipo anati: “Taonani! Mawu a Yehova akhala onyozeka kwa iwo, ndipo sakukondwera nawo. Pakuti aliyense wa iwo, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu akupeza phindu lachinyengo. Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.”—Yeremiya 6:10, 13.
8 Ndi zoona kuti atsogoleriwo ankalimbikitsa anthu awo kuti azipereka nsembe komanso kuchita zinthu zina zokhudza kulambira koona, koma sankachita zinthuzo ndi mtima wonse. Iwo ankakonda kutsatira miyambo m’malo mochita zinthu zoyenera. Komanso atsogoleri Achiyuda ankanamiza anthu kuti aziona ngati zinthu zili bwino n’kumanena kuti: “Kuli mtendere! Kuli mtendere!” pamene kunalibe mtendere. (Yeremiya 6:14; 8:11) Iwo ankachititsa anthu kuti azikhulupirira kuti anali pamtendere ndi Mulungu. Ankaona kuti panalibe vuto lililonse chifukwa anali anthu a Yehova, ankakhala mumzinda woyera komanso anali ndi kachisi. Koma kodi ndi mmenenso Yehova ankaonera?
Yeremiya Yemwe Anali Mneneri Wosadziwika Anapereka Uthenga wa Ziweruzo za Mulungu
9 Yehova anauza Yeremiya kuti apite akaime pachipata cha kachisi kuti azikapereka uthenga wake kwa anthu amene ankalowa m’kachisimo. Iye ankafunika kuwauza kuti: “Musamakhulupirire mawu achinyengo ndi kunena kuti, ‘Nyumba izi ndizo kachisi wa Yehova, inde ndi kachisi wa Yehova, ndithudi ndi kachisi wa Yehova!’ . . . Koma simudzapezapo phindu lililonse.” Ayuda analibe chikhulupiriro, ankangoona zinthu zooneka ndi maso ndipo ankadzitama chifukwa chokhala ndi kachisi. Iwo anali ataiwaliratu mawu a Yehova akuti: “Kumwamba ndiko mpando wanga wachifumu, ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga. Kodi anthu inu mungandimangire nyumba yotani?” Yehova yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa komanso mwini wake wa chilengedwe chonse sakanalephera kuwononga Yerusalemu chifukwa choti kunali kachisi waulemerero.—Yeremiya 7:1-8; Yesaya 66:1.
10 Yeremiya anapitiriza kudzudzula anthuwo kuti: “Kodi mungamabe, kupha, kuchita chigololo, kulumbira monama, kufukiza nsembe zautsi kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunali kuidziwa, . . . n’kumanena kuti, ‘ndithudi tidzapulumutsidwa,’ ngakhale mukuchita zinthu zonyansa zonsezi?” Popeza Ayuda anali mtundu wosankhidwa wa Mulungu, ankaganiza kuti akhoza kumachita zimene akufuna bola ngati akumapereka nsembe ku kachisi. Komatu ngati ankaganiza kuti Yehova ali ngati bambo amene amalekerera mwana wake chifukwa choti ndi mmodzi yekhayo, kunali kusaganiza bwino.—Yeremiya 7:9, 10; Ekisodo 19:5, 6.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
Yeremiya Yemwe Anali Mneneri Wosadziwika Anapereka Uthenga wa Ziweruzo za Mulungu
Ayuda Analangidwa
15 Pofika mu 632 B.C.E., Akasidi ndi Amedi anali atagonjetsa Asuri ndipo mphamvu za Aiguputo zolamulira chigawo chakum’mwera kwa Yuda zinali zitachepa. Ayuda ankayembekezera kuwonongedwa ndi mtundu wochokera kumpoto. Yeremiya anali atachenjeza Ayuda za nkhaniyi kuti: “Taonani! Anthu akubwera kuchokera kudziko la kumpoto. . . . Umenewu ndi mtundu wankhanza ndipo sudzachita chisoni. . . . Mtunduwo wafola pokonzekera kumenya nawe nkhondo ngati mmene mwamuna wankhondo amachitira, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni.” Nthawi imeneyo ulamuliro wamphamvu padziko lonse unali wa Babulo. Ulamuliro umenewu ndi womwe Yehova anaugwiritsa ntchito polanga Ayuda osakhulupirika.—Yeremiya 6:22, 23; 25:8, 9.
MARCH 20-26
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 8-11
it-1-E 555
Nkhaka
Alimi ankaimika zipilala komanso zinthu zina m’minda mwawo pofuna kuthamangitsa nyama. Mneneri Yeremiya anayerekezera mafano amene mitundu ina inkalambira ndi ‘zoopsezera mbalame m’munda wa minkhaka.’—Yer. 10:5.
MARCH 27–APRIL 2
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 12-16
it-1-E 1121 ¶2
Chiuno
Yehova anayerekezera nyumba ya Isiraeli komanso Yuda ndi lamba wa m’chiuno mwake, kutanthauza kuti iye anali nawo pafupi kwambiri. Yehova anachita izi kuti anthuwo azimutamanda komanso kuti akhale chinthu chake chokongola. (Yer. 13:11) Ulosi unaneneratu kuti Yesu Khristu adzalamulira mwachilungamo ndipo chilungamocho ndi kukhulupirika zidzakhala ngati lamba m’chiuno mwake. Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake mwachilungamo komanso mokhulupirika. Mofanana ndi lamba, makhalidwe akewa amamuthandiza kugwira bwino ntchito yake monga Woweruza wosankhidwa ndi Yehova.—Yes. 11:1, 5.