Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya April 2017
APRIL 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 17–21
it-2-E 776 ¶4
Kulapa
Munthu woumba mbiya akhoza kupanga chinthu chinachake kenako n’kuchisintha ngati ‘chawonongeka ndi dzanja la woumbayo.’ (Yer. 18:3, 4) Chitsanzochi, sichikutanthauza kuti Yehova ali ngati munthu amene amaumba mbiya n’kuiwononga ndi dzanja lake. M’malo mwake, zikutanthauza kuti Yehova ali ndi mphamvu yolamulira anthu mwachilungamo komanso mwachifundo ndipo amatha kusintha zochita zake mogwirizana ndi zimene anthu akuchita kapena akulephera kuchita. (Yerekezerani Yes. 45:9; Aroma 9:19-21) Iye angathe kusintha maganizo ake kuti asagwetse tsoka limene anakonza kuti agwetsere mtundu winawake wa anthu kapena kusintha maganizo ake pa zabwino zimene anakonza kuti achite pofuna kuwapindulitsa. Akhoza kuchita zonsezi potengera zimene mtunduwo wachita. (Yer. 18:5-10) Choncho, izi sizikutanthauza kuti Yehova yemwe ndi Woumba Mbiya Wamkulu angalakwitse zinthu. Koma anthu omwe ali ngati “dongo” ndi amene amafunika kusintha kwambiri mitima yawo. Izi ndi zimene zimachititsa kuti Yehova asagwetse tsoka kapena asachite zabwino zimene anakonza.
APRIL 24-30
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 29–31
it-1-E 524 ¶3-4
Pangano
Pangano Latsopano. M’zaka za m’ma 600 B.C.E., Yehova ananeneratu kudzera mwa mneneri Yeremiya za pangano latsopano, kuti lidzakhala losiyana ndi pangano la Chilamulo limene Aisiraeli anaphwanya. (Yer. 31:31-34) Usiku woti afa mawa lake, pa Nisani 14, mu 33 C.E., Yesu anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, ndipo ananena za pangano latsopano lomwe linatheka chifukwa cha magazi ake. (Luka 22:20) Patadutsa masiku 50 kuchokera pamene anaukitsidwa, Yesu anapereka mzimu woyera umene anapatsidwa ndi Yehova kwa ophunzira ake omwe anasonkhana m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu. Apa n’kuti patadutsa masiku 10 kuchokera pamene iye anakwera kumwamba kwa Atate wake.—Mac. 2:1-4, 17, 33; 2 Akor. 3:6, 8, 9; Aheb. 2:3, 4.
M’panganoli muli Yehova ndi “Isiraeli wa Mulungu,” yemwe ndi Akhristu obadwa ndi mzimu ogwirizana ndi Khristu. Amenewa ndi omwe amapanga thupi kapena kuti mpingo wake. (Aheb. 8:10; 12:22-24; Agal. 6:15, 16; 3:26-28; Aroma 2:28, 29) Pangano latsopanoli linayamba kugwira ntchito chifukwa cha magazi amene Yesu Khristu anakhetsa. Yesu anakapereka mtengo wa magazi ake kwa Yehova pamene anakwera kumwamba. (Mat. 26:28) Mulungu akasankha munthu kuti adzapite kumwamba (Aheb. 3:1), amamulowetsa m’panganoli pogwiritsa ntchito nsembe ya Khristu. (Sal. 50:5; Aheb. 9:14, 15, 26) Yesu Khristu ndi Mkhalapakati wa pangano latsopanoli (Aheb. 8:6; 9:15) ndiponso ndi mbali yoyamba ya Mbewu ya Abulahamu. (Agal. 3:16) Popeza kuti Yesu ndi Mkhalapakati wa pangano latsopano, amathandiza anthu a m’panganoli kuti nawonso akhale mbewu yeniyeni ya Abulahamu. (Aheb. 2:16; Agal. 3:29) Yehova amawakhululukira machimo awo ndipo amawaona kuti ndi olungama.—Aroma 5:1, 2; 8:33; Aheb. 10:16, 17.