August 7-13
EZEKIELI 28-31
Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Anapereka Cholowa kwa Anthu Omwe Sankamulambira”: (10 min.)
Ezek. 29:18—Mfumu Nebukadinezara sinalandire malipiro aliwonse pa ntchito yovuta imene inagwira yogonjetsa Turo (it-2 1136 ¶4)
Ezek. 29:19—Mfumu Nebukadinezara inapita kukalanda zinthu za ku Iguputo ngati malipiro chifukwa chogonjetsa Turo (it-1 698 ¶5)
Ezek. 29:20—Yehova anapereka cholowa kwa a Babulo chifukwa choti anachita zinthu zimene iyeyo ankafuna (g86 11/8 27 ¶4-5)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Ezek. 28:12-19—Kodi zochita za mafumu a Turo zikufanana bwanji ndi zochita za Satana? (it-2 604 ¶4-5)
Ezek. 30:13, 14—Kodi ulosi umenewu unakwaniritsidwa bwanji? (w03 7/1 32 ¶1-3)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Ezek. 29:1-12
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Kukambirana “Zitsanzo za Ulaliki.” Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo. Limbikitsani ofalitsa kuti pochita zitsanzo za ulaliki azitchulanso zinthu zimene anthu akuda nazo nkhawa zomwe zangochitika kumene m’deralo ndipo azigwiritsa ntchito kavidiyo kakuti Kodi Mungakonde Kumva Uthenga Wabwino? pogawira kabuku ka Uthenga Wabwino.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zofunika pampingo: (5 min.) Mukhoza kukambirana mfundo zimene tikuphunzira mu Buku Lapachaka. (yb17 35-36)
“Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo—Kudzichepetsa”: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo yakuti Muzipewa Zinthu Zimene Zingawononge Khalidwe Lanu la Kukhulupirika—Kunyada.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 5 ¶1-9
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 20 ndi Pemphero