MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo—Kudzichepetsa
N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZICHEPETSA N’KOFUNIKA?
Kudzichepetsa kumatithandiza kuti tikhale paubwenzi ndi Yehova.—Sal. 138:6
Kudzichepetsa kumatithandiza kuti tizigwirizana ndi anthu ena.—Afil. 2:3, 4
Kunyada kumabweretsa mavuto.—Miy. 16:18; Ezek. 28:17
KODI TINGASONYEZE BWANJI KUDZICHEPETSA?
Tizifunsa malangizo kwa ena ndi kuwagwiritsa ntchito.—Sal. 141:5; Miy. 19:20
Tizikhala okonzeka kuthandiza ena pogwira ntchito zooneka ngati zonyozeka.—Mat. 20:25-27
Tisalole kuti luso kapena udindo wathu zitipangitse kukhala onyada.—Aroma 12:3
Kodi ineyo ndingatani kuti ndizisonyeza kwambiri khalidwe la kudzichepetsa?
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIPEWA ZINTHU ZIMENE ZINGAWONONGE KHALIDWE LANU LA KUKHULUPIRIKA—KUNYADA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi zimene timachita tikapatsidwa malangizo zimasonyeza kuti tili ndi khalidwe lotani?
Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti tikhale odzichepetsa?
Kodi ndi njira zinanso ziti zimene tingasonyezere kuti ndife odzichepetsa?