Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 October tsamba 3
  • Kodi Tingatani Kuti Tiziphunzira Malemba Mwakhama

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingatani Kuti Tiziphunzira Malemba Mwakhama
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Alonjeza Danieli Mphotho Yodabwitsa
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Kodi Mulungu Amakukondanidi?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Buku la Danieli ndi Inu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Kuzindikira Alambiri Oona M’nthaŵi ya Chimaliziro
    Samalani Ulosi wa Danieli!
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 October tsamba 3

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingatani Kuti Tiziphunzira Malemba Mwakhama?

Kodi mumafuna kukhala wokhulupirika mukakumana ndi mayesero ngati mmene Danieli anachitira? Danieli ankaphunzira Mawu a Mulungu kuphatikizapo maulosi ozama mwakhama. (Dan. 9:2) Nanunso mukamaphunzira Baibulo mwakhama, mudzakhalabe okhulupirika. Mudzayamba kukhulupirira kwambiri kuti zimene Yehova walonjeza zidzachitikadi. (Yos. 23:14) Kuphunzira Baibulo mwakhama kungakuthandizeninso kuti muzikonda kwambiri Mulungu ndiponso kuti muzichita zoyenera. (Sal. 97:10) Koma kodi mungayambire pati? Taganizirani mafunso otsatirawa.

Danieli akuphunzira Mawu a Mulungu
  • Kodi ndi zinthu ziti zimene ndiyenera kuphunzira? Muzikonzekera nkhani zonse zimene mukaphunzire kumisonkhano yampingo. Kuti muzipindula ndi kuwerenga Baibulo kwa mlungu uliwonse, muzifufuza mfundo zimene simukuzimvetsa bwino. Ena amasankha kuti aphunzire zinthu monga maulosi a m’Baibulo, makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa, maulendo a umishonale a mtumwi Paulo kapenanso zokhudza chilengedwe. Ngati muli ndi funso pa nkhani inayake, muzililemba n’cholinga choti mudzalifufuze pa ulendo wotsatira.

  • Kodi ndingapeze kuti mfundo za nkhani imene ndikufuna kuphunzira? Onerani vidiyo yakuti Zinthu Zotithandiza Pofufuza Chuma cha M’mawu a Mulungu kuti mupeze mfundo zina. Ndiyeno tayesani kufufuza zokhudza maulamuliro amphamvu padziko lonse oimiridwa ndi zilombo zotchulidwa mu Danieli chaputala 7.

  • Kodi ndiziphunzira kwa nthawi yaitali bwanji? Mukamaphunzira nthawi zonse mudzakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Mukhoza kuyamba ndi kumaphunzira kwa kanthawi kochepa kenako mungamawonjezere pang’onopang’ono nthawi yophunzirayo. Kuphunzira Mawu a Mulungu tingakuyerekezere ndi kufufuza chuma chobisika chimene ukayamba kuchipeza, umafunitsitsa kufufuzabe. (Miy. 2:3-6) Mukamachita zimenezi mudzayamba kukonda kwambiri Mawu a Mulungu ndipo kuphunzira Baibulo kudzangokhala ngati mbali ya moyo wanu.​—1 Pet. 2:2.

    Mungapeze mfundo zina zokuthandizani kuti muzisangalala mukamaphunzira mu Galamukani! ya February 2012, tsamba 18-20.

KODI ZILOMBO ZOTCHULIDWA MU DANIELI CHAPUTALA 7 ZIMAIMIRA CHIYANI?

  • Chilombo chooneka ngati mkango chili ndi mapiko a chiwombankhanga

    Dan. 7:4

  • Chilombo chooneka ngati chimbalangondo chaluma nthiti zitatu

    Dan. 7:5

  • Chilombo chooneka ngati kambuku chili ndi mitu 4 komanso mapiko 4

    Dan. 7:6

  • Chilombo chochititsa mantha chili ndi mano akuluakulu a chitsulo komanso nyanga 10

    Dan. 7:7

FUNSO LOWONJEZERA:

Kodi lemba la Danieli 7:8, 24 linakwaniritsidwa bwanji?

Mutu wa chilombo ukuoneka ndi nyanga yaying’ono yomwe ili ndi maso komanso pakamwa. Nyangayi ikuphuka pakati pa nyanga 10, ndipo ikuthyola nyanga zitatu

ZOTI MUDZAFUFUZE ULENDO WOTSATIRA:

Kodi zilombo zotchulidwa mu Chivumbulutso chaputala 13 zimaimira chiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena