October 16-22
HOSEYA 1-7
Nyimbo Na. 18 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Mumasangalala ndi Chikondi Chokhulupirika Ngati Mmene Yehova Amachitira?”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Hoseya.]
Hos. 6:4, 5—Yehova sanasangalale pamene Aisiraeli anasiya kusonyeza chikondi chokhulupirika (w10 8/15 25 ¶18)
Hos. 6:6—Yehova amasangalala tikamasonyeza chikondi chokhulupirika (w07 9/15 16 ¶8; w07 6/15 27 ¶7)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Hos. 1:7—Kodi ndi liti pamene Yehova anachitira chifundo ndiponso kupulumutsa nyumba ya Yuda? (w07 9/15 14 ¶7)
Hos. 2:18—Kodi vesili linakwaniritsidwa bwanji m’mbuyomu nanga lidzakwaniritsidwa bwanji mtsogolo? (w05 11/15 20 ¶16; g05 9/8 12 ¶2)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Hos. 7:1-16
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) 1 Yoh. 5:3—Kuphunzitsa Choonadi—Muitanireni munthuyo kumisonkhano.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Deut. 30:11-14; Yes. 48:17, 18—Kuphunzitsa Choonadi—Mufotokozereni za webusaiti yathu ya jw.org. (Onani mwb16.08 8 ¶2.)
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) lv 12-13 ¶16-18—Sonyezani mmene tingafikire pamtima wophunzira wathu.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zofunika Pampingo: (15 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Fotokozani mfundo za m’Malemba kwa 5 minitsi pogwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda ya November 15, 2015, tsamba 14. Kenako onetsani vidiyo yakuti Mmene Mungaperekere Zopereka pa Zipangizo za Makono. Pambuyo pake, onetsani tsamba la pa jw.org., lakuti “Mmene Mungaperekere Ndalama Zothandizira Ntchito Yathu ya Padziko Lonse,” ndipo fotokozani njira zimene mungagwiritse ntchito m’dziko lanu.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 8 ¶14-18, komanso tsamba 85-86
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 50 ndi Pemphero