Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 December tsamba 7
  • December 31–January 6

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December 31–January 6
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 December tsamba 7

December 31–January 6, 2019

MACHITIDWE 19-20

  • Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero

  • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • “Mukhale Tcheru ndi Kuyang’anira Gulu Lonse la Nkhosa”: (10 min.)

    • Mac. 20:28​—Akulu ndi amene amaweta nkhosa mumpingo (w11 6/15 20-21 ¶5)

    • Mac. 20:31​—Akulu amapereka thandizo “usana ndi usiku” ngati pakufunikira kutero (w13 1/15 31 ¶15)

    • Mac. 20:35​—Akulu ayenera kukhala odzipereka kwambiri (bt 172 ¶20)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

    • Mac. 19:9​—Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji chitsanzo chabwino pa nkhani yochita khama komanso kusintha ulaliki mogwirizana ndi anthu amene wawapeza? (bt 161 ¶11)

    • Mac. 19:19​—Kodi anthu a ku Efeso anasonyeza chitsanzo chabwino chiti chomwe ifenso tiyenera kutengera? (bt 162-163 ¶15)

    • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

    • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 19:1-20

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. M’patseni mwininyumbayo khadi lodziwitsa anthu za webusaiti yathu.

  • Ulendo Wobwereza Wachitatu: (Osapitirira 3 min.) Sankhani lemba lililonse komanso funso limene mudzakambirane ulendo wotsatira.

  • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) jl mutu 15

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 99

  • Muziphunzitsa Achinyamata Amene Akufuna Kuchita Zambiri Potumikira Yehova: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi akulu amagwira ntchito yofunika iti mumpingo? (Mac. 20:28) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kupitirizabe kuphunzitsa ena? Kodi akulu angatengere bwanji chitsanzo cha Yesu pa nkhani ya mmene ankaphunzitsira atumwi ake? Kodi abale amene akuphunzitsidwa ayenera kukhala ndi mtima wotani? (Mac. 20:35; 1 Tim. 3:1) Kodi akulu angaphunzitse ena zinthu ngati ziti? Kodi akulu ayenera kuwaona bwanji amene akuwaphunzitsa?

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 19 ¶10-16 ndi bokosi lakuti “Kodi Asamariya Anachokera Kuti?”

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

  • Nyimbo Na. 60 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena