Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 May tsamba 2
  • “Sitikubwerera M’mbuyo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Sitikubwerera M’mbuyo”
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Banja Lachikristu Limachitira Zinthu Pamodzi
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
    Galamukani!—2022
  • Yehova Amasamalira Anthu Omwe Akudwala
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Zimene Zili M’magaziniyi
    Galamukani!—2022
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 May tsamba 2

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 4-6

“Sitikubwerera M’mbuyo”

4:16-18

M’bale ali pa oxygen ndipo akuganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano

Tayerekezani kuti mabanja awiri akukhala m’chinyumba chakutha komanso chakalekale. Banja limodzi likuoneka lankhawa kwambiri. Koma chodabwitsa n’choti banja linalo likuoneka losangalala. N’chifukwa chiyani mabanjawa ali osiyana choncho? Banja lachiwirili ndi losangalala chifuwa likudziwa kuti posachedwa lisamukira m’nyumba yabwino.

Ngakhale kuti “chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano,” anthu a Mulungu ali ndi chiyembekezo chomwe chimawathandiza kukhala osangalala. (Aroma 8:22) Mavuto omwe tikukumana nawowa, ngakhale kuti talimbana nawo kwa nthawi yaitali, ndi ‘akanthawi komanso opepuka’ tikawayerekezera ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Choncho tikamaganizira madalitso omwe tidzapeze Ufumu ukadzayamba kulamulira padzikoli, timakhala osangalala komanso sitibwerera m’mbuyo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena